Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 October tsamba 3
  • Muziona Kuti Ubwenzi Wanu Ndi Yehova Ndi Wamtengo Wapatali

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziona Kuti Ubwenzi Wanu Ndi Yehova Ndi Wamtengo Wapatali
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkupeŵeranji Kulambira Mafano?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Peŵani Kulambira Mafano Kwamtundu Uliwonse
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Yehova Ndi Mnzanu Weniweni?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Phunzitsani Ena Kukonda Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 October tsamba 3
Munthu akulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. 1. Akupemphera. Muvi ukuloza kumwamba. 2. Akuwerenga Baibulo. Muvi ukuloza pansi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muziona Kuti Ubwenzi Wanu Ndi Yehova Ndi Wamtengo Wapatali

Atumiki a Yehovafe tili ndi mwayi wapadera. Popeza tinadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa, timapitiriza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye, yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa. Mulungu anatikokera kwa iye kudzera mwa Mwana wake. (Yoh 6:44) Komanso amamvetsera mapemphero athu.​—Sl 34:15.

Kodi tingateteze bwanji ubwenzi wathu ndi Mulungu? Njira imodzi ndi kupewa kuchita zinthu zoipa zimene Aisiraeli ankachita. Atangochita pangano ndi Yehova, anapanga mwana wa ng’ombe wagolide n’kuyamba kumulambira. (Eks 32:7, 8; 1Ak 10:7, 11, 14) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimachita chiyani ndikamayesedwa kuti ndichite zoipa? Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti ndimaona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova ndi wamtengo wapatali?’ Kukonda Atate wathu wakumwamba kudzatithandiza kuti tizipewa zinthu zimene amadana nazo.​—Sl 97:10.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITETEZA UBWENZI WANU NDI YEHOVA (AKL 3:5), KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi kusirira kwa nsanje n’kutani?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kusirira kwa nsanje komanso kulambira mafano?

  • Kodi chigololo ndi kulambira mafano zimagwirizana bwanji?

  • N’chifukwa chiyani abale amene ali ndi udindo mumpingo ayenera kuyesetsa kupeza nthawi yocheza ndi akazi awo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena