CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 4-5
Muzipereka kwa Yehova Zonse Zimene Mungathe
Kukhala osauka sikunkalepheretsa Aisiraeli kukhala pa mtendere ndi Yehova. Ngakhale Aisiraeli osauka kwambiri ankatha kupereka chopereka chovomerezeka kwa Yehova ngati zimene anaperekazo zinali zonse zimene akanakwanitsa. Iwo ankatha kupereka ufa koma Yehova ankafuna kuti ukhale “wosalala,” womwe ankaugwiritsa ntchito akalandira alendo olemekezeka. (Ge 18:6) Masiku anonso, Yehova amalandira ‘nsembe yathu yachitamando’ ngati tikupereka zonse zimene tingathe. Iye amalandira ngakhale kuti ndi zochepa chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu.—Ahe 13:15.
Kodi zimenezi zingakulimbikitseni bwanji ngati simungathe kuchita zimene munkachita poyamba, mwina chifukwa cha matenda kapena uchikulire?