CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 6-7
Nsembe Yosonyeza Kuyamikira
Nsembe zachiyanjano zimene Aisiraeli ankapereka zimatikumbutsa kufunika koyamikira Yehova kudzera m’mapemphero komanso m’makhalidwe athu.—Afi 4:6, 7; Akl 3:15.
Tikamapemphera, kodi tingathokoze Yehova chifukwa cha zinthu ziti?—1At 5:17, 18
Kodi kusonyeza kuti ndife oyamikira kumatithandiza bwanji?
Kodi munthu angamadye bwanji “patebulo la ziwanda,” nanga zimenezi zingasonyeze bwanji kuti munthuyo sayamikira Yehova?—1Ak 10:20, 21