Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 December tsamba 3
  • Timasonyeza Chikondi Tikamachita Zinthu Mogwirizana Ndi Chilango Chochokera kwa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timasonyeza Chikondi Tikamachita Zinthu Mogwirizana Ndi Chilango Chochokera kwa Yehova
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Chilango Chimene Chingabale Chipatso cha Mtendere
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kuchotsa Anthu Osalapa Kumathandiza
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Munthu Amene Mumamukonda Akasiya Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 December tsamba 3

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Timasonyeza Chikondi Tikamachita Zinthu Mogwirizana Ndi Chilango Chochokera kwa Yehova

Kuchotsa munthu mumpingo kumateteza mpingowo komanso kumathandiza munthu wosalapayo. (1Ak 5:6, 11) Tikamachita zinthu mogwirizana ndi chilango chochokera kwa Yehova choterechi, timasonyeza chikondi. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo imeneyi ndi yoona ngakhale kuti chilangochi chimakhala chopweteka kwa onse okhudzidwa, kuphatikizapo achibale a munthuyo komanso a m’komiti yoweruza mlandu?

Chofunika kwambiri n’chakuti timasonyeza kuti timakonda Yehova. Zili choncho chifukwa choti timasonyeza kuti timafuna kuyeretsa dzina lake komanso timaona kuti mfundo zake n’zoyera. (1Pe 1:14-16) Timasonyezanso kuti timakonda munthu amene wachotsedwayo. Chilango chokhwima chimapweteka koma chingabale “chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.” (Ahe 12:5, 6, 11) Koma timasokoneza chilango cha Yehova ngati timachezabe ndi munthu amene wachotsedwa kapena wadzilekanitsa ndi mpingo. Tisaiwale kuti Yehova amalanga anthu ake “pa mlingo woyenera.” (Yer 30:11) Choncho tikamachita zinthu mogwirizana ndi chilango cha Yehova komanso kuchitabe zinthu zokhudza kulambira, timayembekezera kuti tsiku lina munthuyo adzabwerera kwa Atate wathu wachifundo.​—Yes 1:16-18; 55:7.

ONERANI VIDIYO YAKUTI PITIRIZANI KUKHALA OKHULUPIRIKA NDI MTIMA WONSE, KENAKO FUNSANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Pitirizani Kukhala Okhulupirika Ndi Mtima Wonse.’ Gabriella ndi Ben akulira atawerenga kalata imene mwana wawo yemwe wachoka panyumba wawalembera.

    Kodi makolo a Chikhristu zimawapweteka bwanji mwana wawo akasiya Yehova?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Pitirizani Kukhala Okhulupirika Ndi Mtima Wonse.’ Anzawo a Gabriella ndi Ben akuwalimbikitsa pambuyo pamisonkhano.

    Kodi anthu mumpingo angathandize bwanji achibale okhulupirika?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Pitirizani Kukhala Okhulupirika Ndi Mtima Wonse.’ Gabriella akuganizira za nkhani ya kupanduka kwa Kora.

    Kodi ndi nkhani iti ya m’Baibulo imene imasonyeza kuti kukhala okhulupirika kwa Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kukhala okhulupirika kwa achibale athu?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Pitirizani Kukhala Okhulupirika Ndi Mtima Wonse.’ Atachoka kumisonkhano, Gabriella akuuza Ben za meseji imene mwana wawo wawalembera.

    Kodi timasonyeza bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa achibale athu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena