KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Zimene Tinganene
Ulendo Woyamba
Funso: Kodi Mulungu amamvetsera mapemphero athu?
Lemba: Sl 65:2
Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi ndi zinthu ziti zomwe tingatchule m’mapemphero athu?
LEMBALI LIKUPEZEKA MU:
Ulendo Wobwereza
Funso: Kodi ndi zinthu ziti zomwe tingatchule m’mapemphero athu?
Lemba: 1Yo 5:14
Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphero athu?
LEMBALI LIKUPEZEKA MU:
Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso (27 February–27 March)
“Tabwera [kapena takuimbirani kapenanso takulemberani] kuti tikuitanireni kumwambo wofunika kwambiri womwe udzachitike padziko lonse. Mwambo umenewu ndi wokumbukira imfa ya Yesu.” Kenako m’patseni kapepala [kapena mutumizireni meseji kapenanso imelo]. “Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino [kapena zimene mungachite kuti muchite nawo mwambowu pa intaneti]. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani yapadera yomwe idzakambidwe kumapeto a mlungu woyambira March 15.”
Funso la Ulendo Wotsatira Ngati Munthuyo Wasonyeza Chidwi: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?