KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Zimene Tinganene
Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso (27 February–27 March)
“Tabwera [kapena takuimbirani kapenanso takulemberani] kuti tikuitanireni kumwambo wofunika kwambiri womwe udzachitike padziko lonse. Mwambo umenewu ndi wokumbukira imfa ya Yesu.” Kenako m’patseni kapepala [kapena mutumizireni meseji kapenanso imelo]. “Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino [kapena zimene mungachite kuti muchite nawo mwambowu pa intaneti]. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani yapadera yomwe idzakambidwe kumapeto a mlungu woyambira March 15.”
Ngati Munthuyo Wasonyeza Chidwi: Musonyezeni [kapena mutumizireni linki ya] vidiyo yakuti Tizikumbukira Imfa ya Yesu.
Funso la Ulendo Wotsatira: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
Ulendo Woyamba
Funso: Kodi Yesu anali ndani?
Lemba: Mt 16:16
Funso la Ulendo Wotsatira: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
LEMBALI LIKUPEZEKA MU:
Ulendo Wobwereza
Funso: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
Lemba: Mt 20:28
Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe ya dipo ya Yesu?
LEMBALI LIKUPEZEKA MU: