CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Yehova Mulungu Wanu Akufuna Kuti Muzichita Chiyani?”
Tizimvera Yehova chifukwa chomulemekeza kwambiri komanso kumukonda (De 10:12; w09 10/1 10 ¶3-4)
Kumvera kumabweretsa madalitso (De 10:13; w09 10/1 10 ¶6)
Yehova amafuna kuti tikhale naye paubwenzi wolimba (De 10:15; cl 16 ¶2)
Yehova satikakamiza kuti tizimumvera. M’malomwake, iye amafuna kuti tizimukonda komanso kumumvera “mochokera pansi pa mtima.” (Aro 6:17) Anthu amene asankha kutumikira Yehova amakhala moyo wosangalala kwambiri.