Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 January tsamba 11
  • Achinyamata, Muzicheza Momasuka ndi Makolo Anu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata, Muzicheza Momasuka ndi Makolo Anu
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • “Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Zochita Zanu Zingathandize Banja Lanu Kukhala Losangalala
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mungatani Kuti Aliyense Azisangalala M’banja Lanu?​—Mbali Yachiwiri
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 January tsamba 11

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Achinyamata, Muzicheza Momasuka ndi Makolo Anu

N’chifukwa chiyani muyenera kufotokozera makolo anu momasuka zamumtima mwanu? (Miy 23:26) Chifukwa Yehova anawapatsa udindo wokusamalirani komanso wokuyang’anirani. (Sl 127:3, 4) Zikhoza kukhala zowavuta kuti akuthandizeni ngati mungamawabisire zimene mukuganiza kapena zimene zikukudetsani nkhawa. Komanso simungaphunzire chilichonse pa zimene iwo akumana nazo pa moyo wawo. Kodi n’kulakwa kusauza anthu ena zimene ukuganiza? Sikulakwa. Koma kungakhale kulakwa ngati ukuwapusitsa.​—Miy 3:32.

Kodi mungatani kuti muzilankhulana bwino ndi makolo anu? Muzipeza nthawi yabwino kwa inu komanso kwa iwowo. Ngati zingakuvuteni kulankhula nawo, mukhoza kuwalembera kalata yowafotokozera mmene mukumvera. Koma nanga bwanji ngati akufuna kulankhula nanu pankhani imene inuyo simukufuna kukambirana ndi wina aliyense? Muzikumbukira kuti cholinga chawo ndi kukuthandizani. Muziona makolo anu kuti ndi anzanu, osati adani anu. Mukamayesetsa kulankhula ndi makolo anu momasuka, zinthu zidzakuyenderani bwino kwa moyo wanu wonse, ndipo mudzapeza moyo wosatha.​—Miy 4:10-12.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MOYO WANGA WACHINYAMATA​—KODI NDINGATANI KUTI NDIZILANKHULANA BWINO NDI MAKOLO ANGA? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Moyo Wanga Wachinyamata​—Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?” Mtsikana waika mahedifoni m’makutu komanso akugwiritsa ntchito kompyuta ndipo akunyalanyaza mayi ake amene akufuna kulankhula naye.

    Kodi Esther ndi Partik anazindikira zotani zokhudza mmene amachitira zinthu pa moyo wawo?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Moyo Wanga Wachinyamata​—Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?” Mtsikana akucheza ndi mayi ake ndipo akuwasonyeza zinthu zina pafoni yake.

    Kodi mungaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yesu?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Moyo Wanga Wachinyamata​—Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?” Amayi asiya kaye kugwira ntchito zapakhomo kuti asewere ndi mwana wawo wamng’ono.

    Kodi makolo anu akhala akusonyeza bwanji kuti amakukondani?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Moyo Wanga Wachinyamata​—Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?” Kochi wa basketball akujambula papepala mmene timu yake ingasewerere.

    Makolo anu amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino

    Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzilankhulana ndi makolo anu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena