Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 July tsamba 11
  • Zochita Zanu Zingathandize Banja Lanu Kukhala Losangalala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochita Zanu Zingathandize Banja Lanu Kukhala Losangalala
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Uphungu Wanzeru wa Mayi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muzigwiritsa Ntchito Mfundo za M’Baibulo Pothandiza Ana Anu Kuti Zinthu Ziwayendere Bwino
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 July tsamba 11
Zithunzi za muvidiyo yakuti “Muzisangalala M’banja Mwanu.” 1. Ana akuona pamene makolo awo akudya keke. 2. Anawo akuseka pa nthawi ya kulambira kwa pabanja. 3. Mmodzi mwa anawo akuona mayi ake amene akudwala omwe agona pampando.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zochita Zanu Zingathandize Banja Lanu Kukhala Losangalala

Yehova amafuna kuti mabanja azikhala osangalala. (Sl 127:3-5; Mla 9:9; 11:9) Komabe, chimwemwe chathu chikhoza kusokonezedwa chifukwa cha zochitika za m’dzikoli kapena zolakwitsa za anthu a m’banja lathu. Kodi aliyense m’banja angatani kuti athandize kuti banjalo likhale losangalala?

Mwamuna amapereka ulemu kwa mkazi wake. (1Pe 3:7) Amapeza nthawi yocheza naye. Sayembekezera zambiri zoposa zimene mkazi wake angakwanitse ndiponso amasonyeza kuti amayamikira chifukwa cha zimene amamuchitira komanso zimene amachitira banja lake. (Akl 3:15) Amamusonyeza chikondi komanso amamutamanda.​—Miy 31:28, 31.

Mkazi amapeza njira zimene angathandizire mwamuna wake. (Miy 31:12) Amamugonjera komanso amachita naye zinthu mogwirizana. (Akl 3:18) Amalankhula naye mokoma mtima ndiponso amalankhula zabwino zokhudza mwamunayo.​—Miy 31:26.

Makolo amapeza nthawi yocheza ndi ana awo. (De 6:6, 7) Amawauza ana awo kuti amawakonda. (Mt 3:17) Akamawalangiza, amachita nawo zinthu mwachikondi komanso mozindikira.​—Aef 6:4.

Ana amalemekeza komanso amamvera makolo awo. (Miy 23:22) Amawafotokozera zimene akuganiza komanso mmene akumvera. Amamvera malangizo ochokera kwa makolo awo ndipo amawapatsa ulemu.​—Miy 19:20.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZISANGALALA M’BANJA MWANU, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

Kodi aliyense anachita zotani kuti athandize banjali kukhala losangalala?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena