MOYO WATHU WACHIKHRISTU | MUKHALE NDI ZOLINGA MU CHAKA CHAUTUMIKI CHIKUBWERACHI
Samukirani Kumene Kukufunika Olalikira Ufumu Ambiri
Pamafunika chikhulupiriro ngati tikufuna kusamukira kudera latsopano pofuna kuchita zambiri pa utumiki wathu. (Ahe 11:8-10) Ngati muli ndi zolinga zosamukira kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri, mungalankhule ndi akulu a mumpingo mwanu. Kodi mungachite chiyani kuti muwerengere mtengo wake komanso musankhe dera lomwe mungapite? Onani zimene mabuku komanso mavidiyo athu amanena zokhudza kusamukira kumene kukufunika olalikira ambiri. Mungakambirane ndi anthu amene anakwanitsa kusamuka n’kukathandiza mpingo wina. (Miy 15:22) Mungapemphere kwa Yehova kuti akutsogolereni. (Yak 1:5) Mungafufuze zambiri zokhudza dera lomwe mukuganiziralo, ndipo ngati n’zotheka, mungapite kukaonako kwa masiku angapo musanatsimikize zosamukirako.
ONERANI VIDIYO YAKUTI LOWANI PA KHOMO LA UTUMIKI MWACHIKHULUPIRIRO—SAMUKIRANI KUMENE KUKUFUNIKA OLALIKIRA UFUMU AMBIRI, NDIPO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
Kodi Gabriel anakumana ndi mavuto otani, nanga n’chiyani chimene chinamuthandiza?