MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mungapeze Nzeru Zokuthandizani pa JW.ORG
Mawu a Mulungu amatithandiza m’njira zosiyanasiyana kuti tizitha kupirira mavuto omwe tikukumana nawo m’masiku otsiriza ano. (2Ti 3:1, 16, 17) Komabe, nthawi zina timafunikira thandizo kuti tipeze mfundo za m’Baibulo zimene tingazigwiritse ntchito tikakumana ndi vuto linalake. Mwachitsanzo, kodi ndinu kholo ndipo mukufuna malangizo olerera ana? Kodi ndinu wachinyamata amene chikhulupiriro chanu chikuyesedwa? Kodi mudakali ndi chisoni chifukwa mwamuna kapena mkazi wanu anamwalira? Pa jw.org pali nkhani zimene zingakuthandizeni kupeza mfundo za m’Baibulo zomwe ndi zothandiza pothana ndi mavuto ngati amenewa kapena enanso.—Miy 2:3-6.
Mukatsegula tsamba loyamba la webusaiti ya jw.org, dinani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA. (Onani chithunzi 1.) Kenako sankhani zimene mukufuna kuwerenga. Kapena dinani pamene alemba kuti LAIBULALE > NKHANI ZOSIYANASIYANA ndipo sankhani zimene mukufuna kuwerenga. (Onani chithunzi 2.) Nkhanizi mungazipezenso pa JW Library®.a Mwina mungakonde kuti mungoona nkhani zimene zili pamalo amenewa. Njira ina imene ingakuthandizeni kupeza nkhani zimene mukufuna ndi kugwiritsa ntchito malo ofufuzira pa jw.org.
Fufuzani mitu yotsatirayi pogwiritsa ntchito kabokosi kofufuzira kenako mulembe nkhani zimene mukufuna kuwerenga pa mutu umenewo.
Kulera ana
Nkhawa za achinyamata
Imfa ya mwamuna kapena mkazi wanu
a Panopa nkhani zina zikungopezeka pa jw.org pokha.