CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mumachita Zinthu Molimba Mtima Ngati Asa?
Asa anadzipereka poteteza kulambira koona (1Mf 15:11, 12; w12 8/15 8 ¶4)
Molimba mtima, Asa anasonyeza kuti kulambira Yehova kunali kofunika kwambiri kuposa anthu a m’banja lake (1Mf 15:13; w17.03 19 ¶7)
Ngakhale kuti Asa ankalakwitsa zinthu zina, Yehova ankamuonabe kuti anali wokhulupirika chifukwa cha makhalidwe ake abwino (1Mf 15:14, 23; it-1 184-185)
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndimasonyeza kuti ndimakonda kwambiri kulambira koona? Kodi ndimasiya kuchita zinthu ndi wina aliyense, ngakhale wachibale wanga, amene wasiya kutumikira Yehova?’—2Yo 9, 10.