Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 July tsamba 15
  • Tsanzirani Chikondi Chokhulupirika cha Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsanzirani Chikondi Chokhulupirika cha Yehova
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Timapindula Bwanji ndi Chikondi Chokhulupirika cha Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kodi Mumasangalala ndi Chikondi Chokhulupirika Ngati Mmene Yehova Amachitira?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Yehova Amakukondani Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Yehova?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 July tsamba 15

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tsanzirani Chikondi Chokhulupirika cha Yehova

Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chokhulupirika. (Sl 103:11) Chikondi chimenechi sikuti chimangokhalapo kwa kanthawi kochepa kenako n’kutha. Chikondi chokhulupirika chimakhala champhamvu komanso chimakhalitsa. Yehova anasonyeza khalidwe limeneli kwa anthu ake Aisiraeli m’njira zambiri. Iye anawamasula ku ukapolo ku Iguputo ndipo analowetsa m’Dziko Lolonjezedwa. (Sl 105:42-44) Ankawamenyera nkhondo komanso ankawakhululukira mobwerezabwereza akachimwa. (Sl 107:19, 20) Kuchita “chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha, [chikondi chokhulupirika]” kumatilimbikitsa kuti tizimutsanzira.​—Sl 107:43.

Zithunzi za muvidiyo yakuti “Muzichita Chidwi ndi Ntchito za Yehova Zosonyeza Chikondi Chokhulupirika.” 1. M’bale Ben ali ndi m’bale wina ndipo akucheza ndi mlongo kunyumba kwake. 2. M’bale Ben ali kundende limodzi ndi abale ena, ndipo akupereka chakudya kwa m’bale wina amene akudwala ndipo wagona pabedi.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA CHIDWI NDI NTCHITO ZA YEHOVA ZOSONYEZA CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tingasonyeze chikondi chokhulupirika m’njira ziti?

  • N’chifukwa chiyani kusonyeza chikondi chokhulupirika kumafuna kusiya zinthu zina?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena