MOYO WATHU WACHIKHRISTU
‘Mukhale Okhutira Ndi Zimene Muli Nazo Panopa’
Ngati ndife osauka, tikhoza kuyesedwa kuti tichite zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, tikhoza kupeza mwayi wa ndalama zambiri koma umene ungachititse kuti tizilephera kuchita zinthu zauzimu. Kuganizira mfundo za palemba la Aheberi 13:5 kungatithandize.
“Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama”
Muipempherere nkhaniyi ndipo muganizire mofatsa mmene mumaonera ndalama; kodi ana anu mukuwapatsa chitsanzo chotani?—g 9/15 6.
“Koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo”
Mungaonenso, n’kusintha mmene mumaonera zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu. —w16.07 7 ¶1-2.
“Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono”
Muzikhulupirira kuti Yehova adzakuthandizani kupeza zinthu zofunika pa moyo mukapitiriza kuika zinthu zokhudza Ufumu pa malo oyamba.—w14 4/15 21 ¶17.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MMENE ABALE ATHU AKUKHALIRA MWAMTENDERE NGAKHALE KUTI AKUKUMANA NDI MAVUTO AZACHUMA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira Miguel Novoa?