NKHANI YOPHUNZIRA 33
NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka
Kodi Mpingo Ungatsanzire Bwanji Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Anthu Ochimwa?
“Wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza.”—1 YOH. 2:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana zimene tikuphunzirapo pa zimene zinachitika mumpingo wa ku Korinto munthu wina atachita tchimo lalikulu.
1. Kodi Yehova amafuna kuti anthu onse achite chiyani?
YEHOVA anapatsa anthu ufulu wosankha. Timagwiritsa ntchito ufulu umenewu nthawi zonse tikamasankha zochita. Nkhani yofunika kwambiri imene aliyense afunika kusankha ndi yokhudza kudzipereka kwa Yehova n’kukhala m’banja la anthu amene amamulambira. Yehova amafuna kuti munthu aliyense achite zimenezi. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti amakonda anthu ndipo amawafunira zabwino. Iye amafuna kuti akhale nawo pa ubwenzi komanso apeze moyo wosatha.—Deut. 30:19, 20; Agal. 6:7, 8.
2. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene sanalape achite chiyani? (1 Yohane 2:1)
2 Koma Yehova sakakamiza anthu kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha yekha zimene akufuna kuchita. Kodi chimachitika n’chiyani ngati Mkhristu wobatizidwa waphwanya lamulo la Mulungu n’kuchita tchimo lalikulu? Ngati sangalape, ayenera kuchotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:13) Komabe ngakhale zili choncho, Yehova amayembekezera kuti munthu amene wachita zoipayo adzabwerera kwa iye. Ndipotu n’chifukwa chake anapereka dipo kuti anthu ochimwa amene alapa azikhululukidwa. (Werengani 1 Yohane 2:1.) Mulungu wathu wachikondi amapempha anthu amene achita tchimo kuti alape.—Zek. 1:3; Aroma 2:4; Yak. 4:8.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Yehova amafuna kuti tizitsanzira maganizo ake pa nkhani ya machimo komanso anthu amene achita tchimo. Munkhaniyi tikambirana mmene tingachitire zimenezi. Mukamawerenga nkhaniyi muona (1) zimene zinachitika mu mpingo wa ku Korinto munthu wina atachita tchimo lalikulu, (2) malangizo amene mtumwi Paulo anapereka munthu wochimwayo atalapa, komanso (3) mmene nkhani ya m’Baibuloyi ikusonyezera momwe Yehova amaonera Akhristu amene achita tchimo lalikulu.
ZIMENE MPINGO WA KU KORINTO UNACHITA MUNTHU WINA ATACHITA TCHIMO LALIKULU
4. Kodi n’chiyani chinachitika mumpingo wa ku Korinto? (1 Akorinto 5:1, 2)
4 Werengani 1 Akorinto 5:1, 2. Pa ulendo wake wachitatu waumishonale, Paulo anamva nkhani ina yokhumudwitsa yomwe inachitika mumpingo wa ku Korinto womwe unali utangokhazikitsidwa kumene. M’bale wina ankagonana ndi mayi ake omupeza. Khalidweli linali loipa kwambiri moti ‘ngakhale anthu a mitundu ina sankachita.’ Akhristu akumeneko ankaganiza kuti palibe vuto kuti m’bale woteroyo akhalebe mumpingo. Mwina ena ankaganiza kuti izi zimasonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo komanso amawamvetsa anthu omwe si angwiro. Koma Yehova salekerera zoipa pakati pa anthu ake. Pochita zinthu mopanda manyazi chonchi, munthuyo ankawononga mbiri ya mpingo. N’kuthekanso kuti ankasokoneza Akhristu amene ankacheza nawo. Ndiye kodi Paulo analangiza mpingowo kuti utani?
5. Kodi Paulo analangiza mpingo kuti uchite chiyani, nanga ankatanthauza chiyani? (1 Akorinto 5:13) (Onaninso chithunzi.)
5 Werengani 1 Akorinto 5:13. Mouziridwa, Paulo analemba kalata ndipo anapereka malangizo oti munthu wochimwayo achotsedwe mumpingo. Kodi Akhristu okhulupirika ankayenera kuchita naye bwanji munthuyo? Paulo anawauza kuti ‘asiye kugwirizana’ naye. Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Iye anafotokoza kuti lamulo limeneli linkaphatikizapo kuti “ngakhale kudya naye munthu wotereyu” n’kosayenera. (1 Akor. 5:11) Kudya limodzi ndi munthu kungachititse kuti tiyambe kucheza naye. Apa n’zoonekeratu kuti Paulo ankatanthauza kuti Akhristu sankayenera kucheza ndi munthuyo. Zimenezi zikanateteza anthu mumpingo kuti asasokonezedwe ndi makhalidwe ake oipa. (1 Akor. 5:5-7) Kuwonjezera pamenepo, kusiya kucheza naye kukanathandiza munthuyo kuzindikira kuti watalikirana kwambiri ndi Yehova komanso kuti achite manyazi n’kulapa.
Mouziridwa ndi Mulungu, Paulo analemba kalata yopereka malangizo oti achotse mumpingo munthu wosalapa (Onani ndime 5)
6. Kodi Akhristu a ku Korinto komanso munthu yemwe anachimwa anatani atalandira kalata ya Paulo?
6 Atatumiza kalata yake kwa Akhristu a ku Korinto, Paulo ayenera kuti ankaganizira zimene mpingowo ungachite ukalandira kalatayo. Kenako Tito anabwera ndi uthenga umene unamusangalatsa. Akhristuwo analandira bwino kalata yake. (2 Akor. 7:6, 7) Iwo anatsatira malangizo a m’kalatayo. Pasanapite nthawi kuchokera pamene Paulo anatumiza kalata yake, munthu wochimwayo analapa n’kusintha khalidwe lake. Ndipo anayamba kutsatira mfundo zolungama za Yehova. (2 Akor. 7:8-11) Ndiye kodi Paulo analangiza mpingowo kuti uchite chiyani?
ZIMENE MPINGO UNKAFUNIKA KUCHITA NDI MUNTHU YEMWE ANALAPA
7. Kodi kuchotsa mumpingo munthu amene anachita tchimo kunamuthandiza bwanji? (2 Akorinto 2:5-8)
7 Werengani 2 Akorinto 2:5-8. Paulo ananena kuti ‘kudzudzulidwa ndi anthu ambiri chonchi kunali kokwanira kwa munthu ameneyu.’ M’mawu ena tingati chilangochi chinamuthandiza kuti alape.—Aheb. 12:11.
8. Kodi Paulo analangiza mpingo kuti uchite chiyani?
8 Pambuyo pake Paulo analangiza mpingowo kuti: “Mukhululukireni ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza” ndipo “mumutsimikizire kuti mumamukonda.” Onani kuti Paulo ankafuna kuti mpingowo uchite zambiri osati kungomulola kuti abwerere m’gulu la Yehova. Paulo ankafuna kuti zolankhula komanso zochita zawo zimutsimikizire munthuyo kuti amukhululukira ndipo amamukonda. Zimenezi zikanasonyeza kuti iwo amulandiranso mumpingo.
9. N’chifukwa chiyani ena zinkawavuta kukhululukira munthu yemwe analapa?
9 Kodi ena mumpingomo zinkawavuta kulandiranso munthu wochimwa yemwe analapa? Baibulo silinena koma n’kutheka kuti ena analipo. Ndipotu zochita zake zinayambitsa mavuto mumpingo komanso kuchititsa manyazi anthu ena. Enanso ayenera kuti ankaona kuti si chilungamo kulandiranso munthuyo monga m’bale wawo chifukwa iwowo ankayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. (Yerekezerani ndi Luka 15:28-30.) Ndiye n’chifukwa chiyani mpingowo unkafunika kumusonyeza chikondi chenicheni m’bale wawo amene anabwererayu?
10-11. Kodi chikanachitika n’chiyani ngati akulu sukanakhululukira munthu wochimwa yemwe analapa?
10 Taganizirani zimene zikanachitika ngati akulu akanakana kulandiranso munthu wolapayo mumpingo kapenanso ngati pambuyo pobwerera Akhristu anzake akanakana kumusonyeza chikondi. Iye akanakhala ndi “chisoni chopitirira malire.” Akanamaona kuti sangatumikirenso Yehova. Zikanamuvutanso kuti apitirize kukonza ubwenzi wake ndi Mulungu.
11 Choopsa kwambiri ndi chakuti ngati abale ndi alongowo akanakana kukhululukira munthu wolapayo akanasokoneza ubwenzi wawo ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa m’malo motsanzira Yehova yemwe amakhululukira anthu ochimwa omwe alapa, akanatsanzira Satana yemwe ndi wopanda chifundo komanso wankhanza. Iwo akanakhala ngati zida zimene Mdyerekezi akugwiritsa ntchito pofuna kulepheretsa munthuyo kuti ayambirenso kutumikira Yehova.—2 Akor. 2:10, 11; Aef. 4:27.
12. Kodi mpingo ukanatsanzira bwanji Yehova?
12 Ndiye kodi mpingo wa ku Korinto ukanatsanzira bwanji Yehova, osati Satana? Iwo akanachita zimenezi potsanzira mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ochimwa omwe alapa. Taonani zimene olemba Baibulo ena ananena zokhudza Yehova. Davide anati iye ndi “wabwino” ndipo ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Mika analemba kuti: “Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu, amene amakhululukira zolakwa ndi machimo?” (Mika 7:18) Ndipo Yesaya ananena kuti: “Munthu woipa asiye njira yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mtima wonse.”—Yes. 55:7.
13. N’chifukwa chiyani kunali koyenera kubwezeretsa mumpingo munthu yemwe analapa? (Onani bokosi lakuti, “Kodi Ndi Liti Pamene Munthu wa ku Korinto Anabwezeretsedwa?”)
13 Kuti anthu a mumpingo wa ku Korinto atsanzire Yehova, anafunika kulandira munthu wochimwa amene analapa komanso kumutsimikizira kuti amamukonda. Potsatira malangizo a Paulo oti alandirenso munthu wolapayo, mpingo unasonyeza kuti unalidi ‘womvera pa zinthu zonse.’ (2 Akor. 2:9) Ngakhale kuti panali patangopita miyezi yochepa kuchokera pamene anachotsedwa, munthuyo analapa. Choncho panalibe chifukwa chochedwera kumubwezeretsa mumpingo.
TIZITSANZIRA CHILUNGAMO NDI CHIFUNDO CHA YEHOVA
14-15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitika mumpingo wa ku Korinto? (2 Petulo 3:9) (Onaninso chithunzi.)
14 Nkhani imene inachitika ku mpingo wa ku Korintoyi inalembedwa kuti ‘itilangize.’ (Aroma 15:4) Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova salekerera machimo akuluakulu pakati pa anthu ake. Iye saona kuti anthu ochimwa omwe sakulapa ayenera kuchitiridwa chifundo kuti apitirizebe kukhala mumpingo limodzi ndi atumiki ake okhulupirika. Yehova ndi wachifundo koma si wolekerera ndipo mfundo zake sizisintha. (Yuda 4) Ndipotu kulekerera munthu wosalapa sichingakhale chifundo chifukwa zingavulaze anthu ena onse mumpingo.—Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33.
15 Ngakhale zili choncho, timadziwa kuti Yehova safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe. Iye amafuna kupulumutsa anthu ngati n’kotheka. Amasonyeza chifundo kwa anthu amene alapa ndipo amafuna kuti akhale nawonso pa ubwenzi. (Ezek. 33:11; werengani 2 Petulo 3:9.) Choncho pamene munthu wa ku Korintoyo analapa n’kusiya njira yake yoipa, Yehova anagwiritsa ntchito Paulo pouza mpingowo kuti umukhululukire n’kumulandiranso mumpingo.
Mpingo umatsanzira chikondi ndi chifundo cha Yehova polandira anthu omwe abwezeretsedwa (Onani ndime 14-15)
16. Kodi mumamva bwanji mukaganizira mmene nkhani ya Korinto inayendera?
16 Kukambirana zimene zinachitika mumpingo wa ku Korinto kwatithandiza kuona kuti Yehova ndi wachikondi komanso wachilungamo. (Sal. 33:5) Kudziwa zimenezi kumatichititsa kuti tizimutamanda kwambiri. Ndipotu tonsefe ndi anthu ochimwa ndipo timafunika kuti azitikhululukira. Tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa chopereka dipo lomwe limachititsa kuti azitikhululukira. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amakonda anthu ake ndipo amawafunira zabwino.
17. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani zotsatira?
17 Kodi munthu wina akachita tchimo lalikulu masiku ano, akulu angatsanzire bwanji chikondi cha Yehova n’kumuthandiza kuti alape? Kodi mpingo uyenera kuchita bwanji ngati akulu aganiza zochotsa kapena kubwezeretsa munthu? Mafunso amenewa ayankhidwa munkhani zotsatira.
NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima