NKHANI YOPHUNZIRA 12
NYIMBO NA. 119 Tikhale Ndi Chikhulupiriro Cholimba
Pitirizani Kuyenda Motsogoleredwa ndi Chikhulupiriro
“Tikuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro, osati motsogoleredwa ndi zooneka ndi maso.”—2 AKOR. 5:7.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona mmene malangizo a Mulungu angatithandizire tikamasankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri.
1. N’chifukwa chiyani Paulo ankasangalala akaganizira zimene anachita pa utumiki wake?
PA NTHAWI ina mtumwi Paulo ankadziwa kuti anali atatsala pang’ono kuphedwa. Komabe ankasangalala podziwa kuti wachita zonse zimene ankafunika kuchita pa moyo wake. Poganizira zimenezi, iye ananena kuti: “Ndathamanga pa mpikisanowu mpaka pamapeto. Ndakhalabe ndi chikhulupiriro.” (2 Tim. 4:6-8) Paulo ankasankha zochita mwanzeru pa utumiki wake ndipo sankakayikira kuti Yehova akusangalala naye. Nafenso tiyenera kumasankha zinthu mwanzeru kuti Yehova azisangalala nafe. Kodi tingachite bwanji zimenezi?
2. Kodi kuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro kumatanthauza chiyani?
2 Pofotokoza za iyeyo komanso Akhristu ena okhulupirika, Paulo ananena kuti: “Tikuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro, osati motsogoleredwa ndi zooneka ndi maso.” (2 Akor. 5:7) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamenepa? M’Baibulo, nthawi zina mawu akuti “kuyenda” amatanthauza zimene munthu amasankha kuchita pa moyo wake. Munthu akamayenda motsogoleredwa ndi zimene akuona amasankha zinthu pongotengera zimene akuona ndi maso ake, kumva ndi makutu ake komanso mmene akumvera mumtima. Pomwe munthu yemwe amayenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro amadalira Yehova ndipo amasankha zinthu mogwirizana zimene Yehovayo amafuna. Zimene amachita zimasonyeza kuti samakayikira kuti Mulungu adzamudalitsa, komanso kuti zinthu zidzamuyendera bwino akamatsatira malangizo a Yehova opezeka m’Mawu ake.—Sal. 119:66; Aheb. 11:6.
3. Kodi timapeza madalitso otani tikamayenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro? (2 Akorinto 4:18)
3 N’zoona kuti nthawi zina tonsefe timasankha zinthu potengera zimene tikuona kapena kumva. Koma tikamasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu pongotengera zimene taona kapena kumva, tingakumane ndi mavuto aakulu. Tikutero chifukwa chakuti maso ndi mtima wathu zikhoza kutipusitsa. Tingayambe kunyalanyaza zimene Mulungu amafuna kapena malangizo ake. (Mlal. 11:9; Mat. 24:37-39) Koma tikamayenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro tikhoza kumasankha zinthu zomwe ndi ‘zovomerezeka kwa Ambuye.’ (Aef. 5:10) Tikamatsatira malangizo a Mulungu tidzakhala ndi mtendere wamumtima komanso tidzakhala ndi moyo wosangalala. (Sal. 16:8, 9; Yes. 48:17, 18) Ndipo tikapitiriza kuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro tidzapeza moyo wosatha.—Werengani 2 Akorinto 4:18.
4. Kodi tingadziwe bwanji ngati tikusankha zinthu motsogoleredwa ndi chikhulupiriro kapena zooneka ndi maso?
4 Kodi tingadziwe bwanji ngati tikuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro kapena zooneka ndi maso? Tiyenera kudzifunsa mafunso awa: Kodi ndimasankha zochita potengera chiyani? Kodi ndimasankha pongotengera zimene ndikuona basi? Kodi ndimadalira Yehova n’kumatsatira malangizo ake posankha zochita? Munkhaniyi tiona chimene chingatithandize kuti tipitirize kuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro m’mbali zitatu izi: Posankha ntchito, posankha wokwatirana naye komanso gulu la Mulungu likatipatsa malangizo. Pokambirana mbali iliyonse tiziona zimene zingatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru.
TIKAMASANKHA NTCHITO
5. Kodi tiyenera kumaganizira chiyani tikamasankha ntchito?
5 Tonsefe timafuna kuti tizipeza zinthu zofunika pa moyo wathu komanso wa anthu a m’banja lathu. (Mlal. 7:12; 1 Tim. 5:8) Ntchito zina zimakhala za malipiro abwino. Munthu angathe kupeza zofunika pa moyo n’kusunganso ndalama ina yoti adzagwiritse ntchito m’tsogolo. Pomwe ntchito zina zimakhala za malipiro ochepa moti munthu amangokwanitsa kupeza chakudya zovala ndi pogona basi. Mpake kuti tikamasankha ntchito timaganizira ndalama zomwe tingamalandire. Koma ngati munthu atamangoganizira zimenezi zokha, akhoza kukhala munthu amene akuyenda motsogoleredwa ndi zimene akuona.
6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro tikamasankha ntchito? (Aheberi 13:5)
6 Ngati tili ndi chikhulupiriro tidzaganizira mmene ntchito yomwe tingasankhe ingakhudzire ubwenzi wathu ndi Yehova. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ntchitoyi ichititsa kuti ndizichita zimene Yehova amadana nazo?’ (Miy. 6:16-19) ‘Kodi isokoneza kulambira kwanga komanso izichititsa kuti ndizisiyana ndi banja langa kwa nthawi yaitali?’ (Afil. 1:10) Ngati ndi choncho, sizingakhale bwino kuvomera ntchitoyo ngakhale kuti ntchito zikusowa. Chifukwa chakuti tili ndi chikhulupiriro, zimene tingasankhe ziyenera kusonyeza kuti tikukhulupirira kuti Yehova adzatisamalira.—Mat. 6:33; werengani Aheberi 13:5.
7-8. Kodi m’bale wina wa ku South America anasonyeza bwanji kuti akuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro? (Onaninso chithunzi.)
7 M’bale wina wa ku South America dzina lake Javier,a anaona ubwino woyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro. Iye anati: “Ndinafunsira ntchito ina yabwino. Malipiro ake anali kuwirikiza kawiri malipiro omwe ndinkalandira komanso bwenzi ndikusangalala.” Koma Javier ankafunitsitsa atayamba upainiya, ndiye anafotokoza kuti: “Ndinaitanidwa kuti ndikaonane ndi bwana wa kampaniyo. Ndisanakumane ndi bwanayo ndinapemphera, chifukwa ndinkadziwa kuti Yehova ndi amene ankadziwa zimene zinali zabwino kwa ine. Ndinkafuna ntchito yabwino koma sindinkafuna kuti ntchitoyo indilepheretse kukwaniritsa zolinga zanga zauzimu.”
8 Javier anati: “Pokambirana ndi abwanawo anandiuza kuti nthawi zambiri ndizigwira ovataimu. Ndinawauza mwaulemu kuti sindingakwanitse chifukwa nthawi zina ndimafunika kulalikira komanso kusonkhana.” Choncho Javier anakana ntchitoyo. Patangopita milungu iwiri iye anayamba kuchita upainiya. Pambuyo pake chaka chomwecho anapeza ntchito yogwira kwa masiku ochepa. Iye anati: “Yehova anayankha mapemphero anga ndipo anandipatsa ntchito yogwirizana ndi kuchita upainiya. Ndikusangalala kuti ndinapeza ntchito yomwe imandipatsa mpata wambiri wotumikira Yehova komanso abale anga.”
Ngati akufuna kukukwezani pa udindo kuntchito, kodi zimene mungasankhe zidzasonyeza kuti mumakhulupirira kuti Yehova ndi amene amadziwa zomwe zili zabwino kwambiri kwa inu? (Onani ndime 7-8)
9. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Trésor?
9 Kodi tingatani ngati ntchito yomwe tikugwira ikutilepheretsa kusonyeza kuti ndili ndi chikhulupiriro? Zoterezi zinachitikira m’bale wina wa ku Congo dzina lake Trésor. Iye anati: “Ntchito yanga inali yabwino kwambiri. Ndinkalandira malipiro okwera kuwirikiza katatu malipiro omwe ndinkalandira poyamba. Anthu ambiri ankandilemekeza.” Koma nthawi zambiri Trésor ankagwira ovataimu moti sankapezeka pamisonkhano. Nthawi zina ankakakamizidwa kuti abise zinthu zina zachinyengo. Trésor ankafuna kuti asiye ntchitoyo koma ankaopa kuti mwina sapeza ntchito ina. Kodi chinamuthandiza n’chiyani kuti asiye ntchitoyo? Iye anati: “Lemba la Habakuku 3:17-19 linandithandiza kudziwa kuti Yehova akhoza kundisamalira ngakhale ntchito itandithera. Choncho ndinasiya ntchitoyo.” Iye anafotokozanso kuti: “Mabwana ambiri amaganiza kuti munthu akhoza kulolera kuti asakhale ndi nthawi yambiri yocheza ndi banja lake komanso kulambira Mulungu chifukwa cha ntchito ya ndalama zambiri. Ndimasangalala kuti ndinateteza ubwenzi wanga ndi Yehova komanso ndi banja langa. Patapita chaka chimodzi Yehova anandithandiza kupeza ntchito. Inali ya malipiro ochepa koma yomwe inkandipatsa mpata wolambira Mulungu. Tikaika zomwe Yehova amafuna pamalo oyamba, tikhoza kuvutika kwa kanthawi komabe iye adzatisamalira.” Tikamapitiriza kudalira malangizo komanso malonjezo a Yehova, tidzapitiriza kuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro ndipo iye adzatidalitsa.
TIKAMASANKHA WOKWATIRANA NAYE
10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikungoyenda motsogoleredwa ndi zimene tikuona posankha wokwatirana naye?
10 Banja ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo palibe cholakwika ngati munthu akufuna kukhala pabanja. Mlongo angathe kuona m’bale yemwe akuganiza kuti angathe kukwatirana naye ndipo angaganizire zinthu monga khalidwe, maonekedwe ndi mbiri yake ndiponso mmene amapezera ndalama, ngati akusamalira achibale komanso ngati amamusangalatsa.b Zinthu zimenezi ndi zofunika. Koma ngati atamangoganizira zinthu zokhazi, mlongoyo angakhale akuyenda motsogoleredwa ndi zimene akuona.
11. Kodi tingasonyeze bwanji chikhulupiriro posankha wokwatirana naye? (1 Akorinto 7:39)
11 Yehova amasangalala kuona abale ndi alongo akutsatira malangizo ake posankha wokwatirana naye. Mwachitsanzo, iwo amatsatira malangizo ake akuti ayenera kudutsa kaye “pachimake pa unyamata” asanayambe chibwenzi. (1 Akor. 7:36) Akamasankha woti akwatirana naye amaganizira makhalidwe amene Yehova amanena kuti mwamuna kapena mkazi wabwino ayenera kukhala nawo. (Miy. 31:10-13, 26-28; Aef. 5:33; 1 Tim. 5:8) Ngati munthu yemwe si wa Mboni akuwafuna, amatsatira malangizo onena kuti ayenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye,” opezeka pa 1 Akorinto 7:39, (Werengani.) Iwo amapitiriza kuyenda mogwirizana ndi zimene amakhulupirira ndipo sakayikira kuti Yehova yekha ndi amene angawathandize kuti akhale osangalala.—Sal. 55:22.
12. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Rosa?
12 Taganizirani chitsanzo cha Rosa yemwe ndi mpainiya ku Colombia. Kuntchito kwawo ankakumana ndi mwamuna wina yemwe sanali wa Mboni. Mwamunayo anayamba kusonyeza kuti akumufuna ndipo Rosa anayamba kukopeka naye. Rosa anati: “Iye ankaoneka kuti ndi munthu wabwino. Ankagwira ntchito zothandiza anthu a m’dera lake ndipo anali ndi makhalidwe abwino. Ankachita nane zinthu mokoma mtima. Anali ndi makhalidwe onse omwe ndinkafuna kwa mwamuna, kungoti sanali wa Mboni.” Rosa anawonjezera kuti: “Zinali zovuta kumukana chifukwa ndinali nditakopeka naye kale. Pa nthawiyo ndinkasowa wocheza naye ndipo ndinkangofuna nditakwatiwa, koma ndinali ndisanapeze m’bale.” Koma Rosa sankangoganizira zinthu zooneka. Iye anaganizira mmene zosankha zake zingakhudzire ubwenzi wake ndi Yehova. Choncho anasiya kucheza ndi munthuyo ndipo anapitiriza kutumikira Yehova mwakhama. Pasanapite nthawi yaitali Rosa anaitanidwa ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, ndipo panopa ndi mpainiya wapadera. Rosa anati: “Yehova wandithandiza kuti ndikhale wosangalala kwambiri.” Ngakhale kuti si zophweka kuyenda motsogoleredwa ndi zimene timakhulupirira pa nkhani ngati zimenezi, zotsatirapo zake zimakhala zabwino.
GULU LA MULUNGU LIKATIPATSA MALANGIZO
13. N’chiyani chingatilepheretse kusonyeza chikhulupiriro gulu la Mulungu likamatipatsa malangizo?
13 Nthawi zambiri timalandira malangizo okhudza kulambira kwathu kuchokera kwa akulu, oyang’anira dera, ofesi ya nthambi kapena Bungwe Lolamulira. Koma nthawi zina sitingamvetse chifukwa chake tapatsidwa malangizo enaake. Zikatero tikhoza kumangoona mavuto amene angabwere chifukwa cha malangizowo. Tikhozanso kumaganizira kwambiri zimene abale omwe apereka malangizowo amalakwitsa.
14. Kodi n’chiyani chingatithandize kuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro gulu la Mulungu likatipatsa malangizo? (Aheberi 13:17)
14 Tikakhala ndi chikhulupiriro sitikayikira kuti Yehova akutsogolera gulu lake ndipo akudziwa mmene zinthu zilili. Choncho timakhala okonzeka kumvera mosanyinyirika. (Werengani Aheberi 13:17.) Timazindikira kuti kumvera kwathu kumathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana. (Aef. 4:2, 3) Ngakhale kuti abale amene amatitsogolera si angwiro, timakhulupirira kuti Yehova adzatidalitsa tikakhala omvera. (1 Sam. 15:22) Ngati pali vuto, timadziwa kuti adzalikonza pa nthawi yake.—Mika 7:7.
15-16. N’chiyani chinathandiza m’bale wina kuti aziyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro ngakhale kuti ankakayikira malangizo omwe anapatsidwa? (Onaninso chithunzi.)
15 Zimene zinachitika ku Peru zimasonyeza ubwino woyenda ndi chikhulupiriro. Ngakhale kuti Chisipanishi ndi chofala m’dzikolo, anthu ambiri amayankhula zinenero zina za kumeneko monga Chikechuwa. Kwa zaka zambiri, abale ndi alongo olankhula Chikechuwa ankafufuza m’gawo lawo anthu olankhula chinenerochi. Gulu la Mulungu linapereka malangizo atsopano olalikirira n’cholinga choti agwirizane ndi malamulo a boma pa nthawiyo. (Aroma 13:1) Ena ankakayikira ngati imeneyo inali njira yothandiza. Koma abale atatsatira malangizo atsopanowa, Yehova anawadalitsa ndipo anayamba kupeza anthu ambiri olankhula Chikechuwa.
16 Kevin yemwe ndi mkulu mumpingo wa Chikechuwa, nayenso ankada nkhawa. Iye anati: “Ndinkadzifunsa kuti, ‘Ndiye tizipeza bwanji anthu olankhula Chikechuwa?’” Kodi Kevin anatani? Iye anati: “Ndinaganizira lemba la Miyambo 3:5 komanso nkhani ya Mose. Yehova anapatsa Mose malangizo omwe ankaoneka ngati osamveka. Anamuuza kuti atsogolere Aisiraeli pochoka ku Iguputo kulowera ku Nyanja Yofiira. Ndipo pamene Aiguputo ankawatsatira, zinkaoneka kuti alibe kolowera. Koma Mose anamvera ndipo Yehova anawadalitsa pochita zinthu zodabwitsa kwambiri.” (Eks. 14:1, 2, 9-11, 21, 22) Kevin anali wokonzeka kumvera. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iye anati: “Ndinadabwa ndi mmene Yehova anatidalitsira. M’mbuyomu tinkatha kuyenda mtunda wautali koma kungopeza munthu mmodzi kapena awiri olankhula Chikechuwa. Panopa timapita kumagawo amene kuli anthu ambiri olankhula chinenerochi. Zimenezi zachititsa kuti tizikambirana ndi anthu ambiri ndiponso tikhale ndi maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo ambiri. Pamisonkhano yathu pamabweranso anthu ambiri.” Kunena zoona Yehova amatidalitsa kwambiri tikamayenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro.
Anthu ambiri amene abale ankakumana nawo ankawauza komwe angapeze anthu ena olankhula Chikechuwa (Onani ndime 15-16)
17. Kodi taphunzira chiyani munkhaniyi?
17 Taona mmene tingasonyezere chikhulupiriro m’njira zitatu. Koma tiyenera kupitiriza kuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro m’mbali zonse za moyo wathu monga posankha zosangalatsa, maphunziro komanso mmene tingalerere ana. Tikamafuna kusankha zochita, tisamangoganizira zimene tikuona koma tiziganizira zokhudza ubwenzi wathu ndi Yehova, malangizo ake komanso lonjezo lake loti adzatisamalira. Tikatero tidzapitiriza ‘kuyenda mʼdzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale.’—Mik. 4:5.
NYIMBO NA. 156 Ndi Maso a Chikhulupiro
a Mayina ena asinthidwa.
b Ndimeyi ikunena za mlongo yemwe akufuna mwamuna. Koma malangizowa angathandizenso m’bale yemwe akufuna mkazi.