MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Zithunzi Zingakuthandizeni
Mabuku athu amakhala ndi zithunzi zomwe zingakuthandizeni kudziwa mfundo zofunika. Kodi mungatani kuti zithunzi zimenezi zizikuthandizani?
Muziona zithunzi musanawerenge nkhani yake. Zithunzi zimachititsa chidwi ndipo zingakulimbikitseni kuti muwerenge nkhaniyo. Zimakhala ngati “mwalawa” zimene mukufuna kuwerengazo. Choncho muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuona chiyani?’—Amosi 7:7, 8.
Mukamawerenga nkhani muzidzifunsa chifukwa chake aikamo chithunzi. Muziwerenga mawu ofotokozera chithunzi ngati alipo. Muziona kugwirizana pakati pa chithunzicho ndi nkhaniyo komanso mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuphunzira.
Mukamaliza kuwerenga, muzionanso zithunzizo kuti mukumbukire mfundo zazikulu. Muziyesa kuonanso chithunzicho m’maganizo mwanu komanso mfundo imene munaphunzirapo.
Tayesani kuonanso zithunzi za m’magazini ino n’kuona ngati mukukumbukira zimene munaphunzira.