NKHANI YOPHUNZIRA 30
NYIMBO NA. 97 Mawu a Mulungu Amatithandiza Kukhala ndi Moyo
Kodi Mfundo Zoyambirira za M’Baibulo Zingakuthandizenibe Masiku Ano?
“Ndikufuna kuti ndizikukumbutsani zinthu zimenezi nthawi zonse, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba mʼchoonadi.”—2 PET. 1:12.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zoyambirira za m’Baibulo zomwe tinaphunzira titangoyamba kumene choonadi.
1. Kodi mfundo za m’Baibulo zinakuthandizani bwanji mutangoyamba kuphunzira choonadi?
MFUNDO zoyambirira za m’Baibulo zinatithandiza kwambiri pa moyo wathu. Mwachitsanzo, titangodziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova tinayesetsa kuti akhale mnzathu. (Yes. 42:8) Titadziwa zimene zimachitika munthu akamwalira sitimaderanso nkhawa ngati okondedwa athu omwe anamwalira akuvutika. (Mlal. 9:10) Ndipo titaphunzira zimene Mulungu walonjeza zokhudza Paradaiso, sitimaderanso nkhawa zokhudza tsogolo lathu. Tinadziwa kuti tingathe kukhala ndi moyo, osati kwa nthawi yochepa ngati zaka 70 kapena 80, koma mpaka kalekale.—Sal. 37:29; 90:10.
2. Kodi lemba la 2 Petulo 1:12, 13, likusonyeza bwanji kuti mfundo zoyambirira zimathandizanso Akhristu omwe atumikira Yehova kwa nthawi yaitali?
2 Sitiyenera kuiwala kufunika kwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Kalata yake yachiwiri, mtumwi Petulo amalembera Akhristu omwe anali kale “olimba m’choonadi.” (Werengani 2 Petulo 1:12, 13.) Koma tsopano iwo ankakumana ndi mavuto ena mumpingo, kuphatikizapo aphunzitsi abodza komanso anthu oipa. (2 Pet. 2:1-3) Petulo ankafuna kulimbikitsa abale ndi alongo ake kuti athe kulimbana ndi mavuto amenewa. Choncho iye anawakumbutsa za zinthu zimene anaphunzira kale poyamba. Mfundo zimenezi zikanawathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova mpaka mapeto.
3. N’chifukwa chiyani Akhristu onse ayenera kumaganizira mfundo zoyambirira za m’Baibulo? Fotokozani.
3 Mfundo zoyambirira za m’Baibulo zingatithandizedi ngakhale kuti takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali. Tiyerekezere motere: Katswiri wodziwa kuphika komanso munthu yemwe akungophunzira kumene angagwiritse ntchito zinthu zofanana pokonza chakudya. Koma katswiriyu yemwe wakhala akuphika kwa nthawi yaitali, amakhala ataphunzira kugwiritsa ntchito zipangizozo pokonza chakudya chokoma m’njira zosiyanasiyana. Mofanana ndi zimenezi, atumiki a Yehova omwe akhala akumutumikira kwa nthawi yaitali ndi ophunzira Baibulo atsopano, akhoza kumaona mfundo zoyambirira za m’Baibulo mosiyana. Zinthu pa moyo wathu kapena zimene takhala tikuchita potumikira Yehova, zimakhala zikusintha kungochokera pamene tabatizidwa. Tikamaganizira mfundo za m’Baibulo zomwe tinaziphunzira kalekale, tingapeze mfundo zatsopano zomwe zingatithandize mogwirizana ndi mmene zinthu zilili panopa. Tiyeni tione zimene Akhristu amene akhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali angaphunzire pa mfundo zitatu zoyambirira za m’Baibulo.
YEHOVA NDI MLENGI
4. Kodi kudziwa kuti Yehova ndi Mlengi kumatithandiza bwanji?
4 Baibulo limati “amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheb. 3:4) Timadziwa kuti dziko lapansili ndi zamoyo zonse, zinalengedwa ndi Mlengi wanzeru komanso wamphamvuyonse. Iye ndi amene anatipanga ndipo amatidziwa bwino kwambiri. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti amatisamalira. Iye amadziwanso zimene ndi zabwino kwambiri kwa ife. Kudziwa mfundo yosavuta ya choonadi yakuti Yehova ndi Mlengi, kumatithandiza m’njira zambiri ndipo kumachititsa kuti tikhale ndi moyo wabwino.
5. Kodi ndi mfundo ya choonadi iti imene ingatithandize kukhala odzichepetsa? (Yesaya 45:9-12)
5 Mfundo yakuti Yehova ndi Mlengi, ingatiphunzitse kukhala odzichepetsa. Mwachitsanzo, pamene Yobu ankangoganizira za iye yekha komanso anthu ena, Yehova anamukumbutsa kuti iye ndi Mlengi wamphamvuyonse. (Yobu 38:1-4) Zimenezi zinamukumbutsa Yobu kuti njira za Yehova ndi zapamwamba kwambiri kuposa za anthu. Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, pambuyo pake mneneri Yesaya analemba kuti: “Kodi dongo lingafunse woumba mbiya kuti: ‘Kodi ukupanga chiyani?’”—Werengani Yesaya 45:9-12.
6. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe n’zofunika kuganizira za Mlengi wathu wanzeru komanso wamphamvuyonse? (Onaninso zithunzi.)
6 Nthawi zina munthu yemwe wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri angayambe kudalira nzeru zake, m’malo modalira Yehova ndi Mawu ake kuti azimutsogolera. (Yobu 37:23, 24) Koma bwanji ngati munthu ataganizira nzeru zopanda malire komanso mphamvu zimene Mlengi ali nazo? (Yes. 40:22; 55:8, 9) Mfundo ya choonadi imeneyi ingamuthandize kukhala wodzichepetsa, n’kumaona kuti maganizo a Yehova ndi olondola komanso ofunika kwambiri.
Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziona kuti maganizo a Yehova ndi abwino kwambiri kuposa athu? (Onani ndime 6)d
7. Kodi n’chiyani chinathandiza Rahela kuti avomereze kusintha komwe kunachitika?
7 Rahela yemwe amakhala ku Slovenia, anaona kuti kuganizira zokhudza Mlengi wake kunamuthandiza kuvomereza kusintha kumene kunachitika m’gululi. Rahela anavomereza kuti: “Nthawi zina zinkandivuta kuvomereza zimene abale otsogolera asankha. Mwachitsanzo, ngakhale pambuyo poonera Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 8 la 2023, zinandionekera zachilendo kuona kwa nthawi yoyamba m’bale wandevu akukamba nkhani. Choncho ndinapempha Yehova kuti andithandize kuvomereza kusintha kumeneku.” Rahela anazindikira kuti Yehova yemwe ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, nthawi zonse amadziwa bwino mmene angatsogolere gulu lake. Ngati inunso nthawi zina zimakuvutani kuvomereza malangizo atsopano kapena kusintha komwe kwachitika, mungachite bwino kudzichepetsa n’kumaganizira mphamvu komanso nzeru zapamwamba za Mlengi wathu.—Aroma 11:33-36.
CHIFUKWA CHAKE MULUNGU AMALOLA KUTI ANTHU AZIVUTIKA
8. Kodi kudziwa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika kumatithandiza bwanji?
8 N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika? Chifukwa cholephera kupeza yankho la funso limeneli, anthu ena amakwiyira Mulungu kapenanso kuyamba kuona kuti kulibeko n’komwe. (Miy. 19:3) Mosiyana ndi anthu amenewa, inuyo mwaphunzira kuti uchimo umene tinatengera ndi womwe umachititsa kuti anthu azivutika, osati Yehova. Mwaphunziranso kuti kuleza mtima kwa Yehova kwathandiza kuti anthu ambiri amudziwe komanso kudzionera okha mmene Yehova adzathetsere mavuto onse mpaka kalekale. (2 Pet. 3:9, 15) Mfundo za choonadi zimenezi zimakulimbikitsani komanso kukuthandizani kuti mukhale naye pa ubwenzi wolimba.
9. Kodi ndi pa nthawi ziti pomwe tingafunike kukumbukira chifukwa chake Yehova walola kuti anthu azivutika?
9 Timadziwa kufunika kokhala oleza mtima pamene tikuyembekezera Yehova kuti adzathetse mavuto. Koma anthu amene timawakonda akamakumana ndi mavuto, zopanda chilungamo kapenanso akamwalira, tingayambe kuona kuti Yehova akuchedwa kuthetsa mavuto. (Hab. 1:2, 3) Pa nthawi ngati zimenezi, tingachite bwino kuganizira zifukwa zimene Yehova walolera kuti anthu olungama azivutika.a (Sal. 34:19) Tiziganiziranso za cholinga chake chodzathetseratu mavuto onse mpaka kalekale.
10. Kodi n’chiyani chinathandiza Anne kuti apirire mayi ake atamwalira?
10 Kudziwa chifukwa chake Yehova walola kuti anthu azivutika kumatithandiza kupirira. Anne yemwe amakhala pachilumba cha Mayotte panyanja ya Indian Ocean, ananena kuti: “Mayi anga atamwalira zaka zingapo zapitazo, ndinakhumudwa kwambiri. Komabe nthawi zonse ndinkadzikumbutsa kuti, si Yehova amene amachititsa kuti anthu azivutika. Iye amafunitsitsa kudzathetsa mavuto onse komanso kudzaukitsa okondedwa athu amene anamwalira. Kuganizira mfundo za choonadi zimenezi, kumandipatsa mtendere wamumtima womwenso umandidabwitsa.”
11. Kodi kuganizira zifukwa zimene zachititsa Yehova kulola kuti anthu azivutika kumatithandiza bwanji kuti tipitirize kulalikira?
11 Kudziwa chifukwa chake Yehova walola kuti anthu azivutika kumatilimbikitsa kuti tipitirize kulalikira. Atafotokoza kuti kuleza mtima kwa Yehova kudzathandiza kuti anthu olapa apulumuke, Petulo analemba kuti: “Ganizirani za mtundu wa anthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.” (2 Pet. 3:11) Kulalikira ndi imodzi mwa ‘ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.’ Mofanana ndi Atate wathu, ifenso timakonda anthu. Timafuna kuti iwonso adzalowe m’dziko latsopano la Mulungu lomwe mudzakhale chilungamo. Moleza mtima, Yehova akupereka mwayi kwa anthu a m’dera lanu woti ayambe kumulambira. Ndi mwayitu waukulu kwambiri kukhala anzake a Mulungu, n’kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti adziwe zokhudza iye mapeto asanafike.—1 Akor. 3:9.
TIKUKHALA ‘M’MASIKU OTSIRIZA’
12. Kodi kudziwa kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ kumatithandiza bwanji?
12 Baibulo limafotokoza molondola zokhudza khalidwe la anthu ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Tim. 3:1-5) Timangofunika kuona mmene zinthu zilili kumene timakhala kuti tione mmene ulosi umenewu ukukwaniritsidwira. Tikamaona makhalidwe a anthu akuipiraipira, zimatithandiza kuti tiyambe kukhulupirira kwambiri kuti Mawu a Mulungu ndi odalirika.—2 Tim. 3:13-15.
13. Mogwirizana ndi fanizo la Yesu la pa Luka 12:15-21, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
13 Kudziwa kuti tikukhala m’masiku otsiriza, kumatithandizanso kuti tiziona kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti. Tiyeni tione zimene tikuphunzira pa mfundo imeneyi kuchokera mufanizo la Yesu la pa Luka 12:15-21. (Werengani.) N’chifukwa chiyani munthu wachuma wa m’fanizoli anatchedwa “wopanda nzeru”? Sikuti anatero chifukwa chakuti munthuyo anali wolemera koma chifukwa chakuti sankaika zinthu zofunika pa malo oyamba. Iye ‘anadziunjikira chuma, koma sanali wolemera kwa Mulungu.’ N’chifukwa chiyani munthuyo ankafunika kuchitapo kanthu mwamsanga? Chifukwa Mulungu anamuuza kuti: “Usiku womwe uno moyo wako aufuna.” Masiku ano, pamene mapeto adzikoli akuyandikira, tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolinga zanga zimasonyeza kuti ndimaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani? Kodi ndimathandiza ana anga kukhala ndi zolinga zotani? Kodi ndimagwiritsa ntchito mphamvu, nthawi komanso chuma changa podziunjikira chuma, kapena ndimasunga chuma changa kumwamba?’
14. Kodi chitsanzo cha Miki chikusonyeza bwanji kuti ndi nzeru kumaganizira umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza?
14 Kuganizira umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiriza, kungatithandize kuti tisankhe zoyenera kuchita pa moyo wathu. Izi ndi zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Miki. Iye anati: “Nditamaliza sukulu, ndinkafunitsitsa nditachita maphunziro okhudza zinyama. Ndinalinso ndi cholinga chofuna kudzachita upainiya komanso kukatumikira kumene kukufunika olalikira ambiri. Anzanga olimba mwauzimu anandithandiza kuti ndiganizire mosamala ngati zinali zofunikadi kuti ndikachite maphunziro apamwamba aja koma n’kukhalabe ndi zolinga zauzimu. Iwo anandikumbutsa kuti posachedwapa mapeto adzikoli afika. Iwo anandikumbutsanso kuti m’dziko latsopano ndidzakhala ndi mwayi wophunzira zokhudza zinyama mpaka kalekale. Choncho ndinasankha kuchita maphunziro a nthawi yochepa. Zimenezi zinandithandiza kupeza ntchito imene ingandithandize kupeza zofunika kwinaku ndikuchita upainiya ndipo kenako ndinasamukira ku Ecuador, komwe kukufunika olalikira ambiri.” Panopa Miki ndi mwamuna wake akutumikira monga oyang’anira dera m’dzikolo.
15. Kodi anthu ena amatani akamva uthenga wabwino? Perekani chitsanzo. (Onaninso zithunzi.)
15 Sitiyenera kugwa ulesi ngati anthu akukana kumvetsera uthenga wabwino. Tikutero chifukwa anthu amatha kusintha. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yakobo yemwe anali mchimwene wake wa Yesu. Iye anaona Yesu akukula n’kukhala Mesiya komanso akuphunzitsa kuposa munthu aliyense. Koma kwa zaka zambiri, Yakobo sanakhale wotsatira wa Yesu. Iye anakhala wotsatira wa Yesu komanso wakhama pambuyo poti Yesuyo waukitsidwa.b (Yoh. 7:5; Agal. 2:9) Choncho tisamasiye kulalikira achibale athu omwe poyamba sakusonyeza chidwi ndipo tizibwerera kwa anthu amene akana kumvetsera uthenga wa Ufumu. Tizikumbukira kuti tikukhala m’masiku otsiriza ndipo ntchito yathu yolalikira ikufunika kugwiridwa mwamsanga. N’kutheka kuti zimene tingawauze panopa angadzazikumbukire m’tsogolo n’kuchitapo kanthu, mwinanso chisautso chachikulu chitayamba.c
Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizilalikirabe achibale athu omwe si a Mboni? (Onani ndime 15)e
TIZIYAMIKIRA ZIKUMBUTSO ZA YEHOVA
16. Kodi zikumbutso za Yehova zimakuthandizani bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “Muzizigwiritsa Ntchito Pothandiza Ena.”)
16 China mwa chakudya chauzimu chimene timalandira chimakonzedwera anthu amene sanamvepo mfundo zoyambirira za choonadi. Mwachitsanzo, nkhani za onse zomwe zimakambidwa mlungu uliwonse, nkhani ndi mavidiyo ena za pa jw.org komanso magazini ogawira, kwenikweni zimakonzedwera anthu omwe si a Mboni. Ngakhale zili choncho, ifenso timapindula ndi zinthu zimenezi. Zimatithandiza kuti tizikonda kwambiri Yehova, tizikhulupirira Mawu ake komanso tiziphunzitsa ena mogwira mtima mfundo zoyambirira za choonadi.—Sal. 19:7.
17. Kodi ndi pa nthawi ziti pomwe tingafunike kuganizira mfundo zoyambirira za m’Baibulo?
17 Kwa amene takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali, timasangalala tikamva mfundo zina za choonadi zomwe zasintha. Koma timayamikiranso kwambiri mfundo za choonadi zofunika zomwe tinaphunzira, zimene zinatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ngati nthawi zina timakakamira maganizo athu, m’malo motsatira malangizo a gulu la Yehova, tizidzichepetsa n’kumakumbukira kuti Mlengi wathu yemwe ndi wamphamvu komanso wanzeru ndi amene akutsogolera gululi. Ifeyo kapena anthu amene timawakonda akamapirira mayesero enaake, tizileza mtima n’kumaganizira chifukwa chake Yehova walola kuti anthu azivutika. Tikamasankha mmene tingagwiritsire ntchito nthawi ndi chuma chathu, tizikumbukira kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Tiyeni tizilola kuti zikumbutso za Yehova zizitithandiza kukhala anzeru komanso kupitirizabe kumutumikira mokhulupirika.
NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe
a Onani nkhani yakuti “Mavuto Onse Atha Posachedwa” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2007, tsamba 21-25.
c Onani nkhani yakuti “Kodi Tikudziwa Chiyani pa Nkhani ya Mmene Yehova Adzaweruzire Anthu?” mu Nsanja ya Olonda ya May 2024, tsamba 8-13.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Bungwe la akulu silinatsatire maganizo a mkulu wina. Pambuyo pake ali kunyumba, mkuluyo akuyang’ana nyenyezi kumwamba ndipo zikumuthandiza kuti ayambe kuona moyenera maganizo ake aja.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pambuyo pophunzira payekha n’kufufuza umboni wotsimikizira kuti tili m’masiku otsiriza, mlongo akuimbira foni mchemwali wake kuti amulalikire.