MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Malifalensi a Malemba Angakuthandizeni
Malifalensi a m’Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika amasonyeza kuti mbali zosiyanasiyana za Baibulo ndi zogwirizana, pokuthandizani kupeza malemba ena omwe ali ndi mfundo zowonjezereka pa nkhani imene mukuwerenga. Malifalensiwa ndi tizilembo ting’onoting’ono tomwe timapezeka kutsogolo kwa liwu. Mu Baibulo losindikizidwa mungapeze tizilembo tofanana nato mudanga lapakati kuti mupeze malemba ena omwe ali ndi nkhani yofanana nayo. Pa jw.org kapena pa JW Library® dinani kachilemboko kuti muone malemba ena.
Malifalensi angakuthandizeni kupeza zinthu monga:
Nkhani Yofanana Nayo: Lifalensi ingakutengereni ku malemba ena omwe ali ndi nkhani ina yofanana ndi nkhani yomwe mukuwerengayo. Mwachitsanzo, onani lemba la 2 Samueli 24:1 ndi 1 Mbiri 21:1.
Komwe Mawu Enaake Achokera: Lifalensi ingakuthandizeni kudziwa kumene mawu ena atengedwa. Mwachitsanzo, onani lemba la Mateyu 4:4 ndi Deuteronomo 8:3.
Kukwaniritsidwa kwa Ulosi: Lifalensi ingakuthandizeni kudziwa mmene ulosi winawake unakwaniritsidwira. Mwachitsanzo, onani lemba la Mateyu 21:5 ndi Zekariya 9:9.