NKHANI YOPHUNZIRA 39
NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”
‘Anthu a Maganizo Abwino’ Adzamvetsera
“Anthu onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.”—MAC. 13:48.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana kufunika kopempha anthu kuti tiziphunzira nawo Baibulo komanso kuti azipezeka pamisonkhano.
1. Kodi zochita za anthu zimasiyana bwanji akamva uthenga wabwino? (Machitidwe 13:47, 48; 16:14, 15)
M’NTHAWI ya atumwi, anthu ambiri ankasangalala akamva uthenga wabwino. (Werengani Machitidwe 13:47, 48; 16:14, 15.) Masiku anonso anthu ena amasangalala akangomva uthenga wabwino koyamba. Ndiye pali ena amene poyamba safuna kumvetsera koma kenako amasintha n’kumafuna kuphunzira. Kodi tizitani tikapeza ‘anthu a maganizo abwino’?
2. Kodi ntchito yathu yophunzitsa anthu imafanana bwanji ndi ya mlimi?
2 Tingayerekezere ntchito yophunzitsa anthu ndi zimene mlimi amachita. Ngati zipatso zina m’munda zapsa, iye amazikolola ngakhale kuti akupitiriza kulima kapena kudzala mbewu zina. Ifenso tikapeza munthu amene akufuna kuphunzira Baibulo, tizimuthandiza mwamsanga kuti akhale wophunzira wa Khristu. Koma anthu amene sanasonyeze chidwi, timapitiriza kuwathandiza kuti aone kufunika kwa zimene tikuwaphunzitsa. (Yoh. 4:35, 36) Kuzindikira kungatithandize kupeza njira yabwino yothandizira munthu aliyense. Tiyeni tikambirane zimene tingachite tikapeza anthu achidwi komanso mmene tingawathandizire.
TIKAPEZA ANTHU AMENE AKUFUNA KUMVETSERA
3. Kodi tizichita chiyani tikakumana ndi anthu amene akufuna kumvetsera? (1 Akorinto 9:26)
3 Tikapeza anthu achidwi, tiyenera kuwathandiza nthawi yomweyo kuti ayambe kuyenda pa njira yopita ku moyo wosatha. Tiziwapempha pa ulendo woyamba womwewo kuti tiyambe kuphunzira nawo Baibulo komanso kuti azipezeka pamisonkhano.—Werengani 1 Akorinto 9:26.
4. Fotokozani chitsanzo cha munthu yemwe ankafuna kuyamba kuphunzira Baibulo pa ulendo woyamba.
4 Tiziwapempha kuti tiyambe kuphunzira. Anthu ena amene timawalalikira amakhala okonzeka kuyamba kuphunzira nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, mlongo wina wa ku Canada akulalikira pakashelefu, mtsikana wina anabwera kudzatenga kabuku kakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale. Mlongoyo atauza mtsikanayo kuti akhoza kumaphunzira naye kabukuko, iye anachita chidwi ndipo anapatsana manambala a foni. Tsiku lomwelo masana, mtsikanayo analembera meseji mlongoyo yomufunsa tsiku limene ayambe kuphunzira. Mlongoyo atanena kuti apitako Loweruka kapena Lamlungu, mtsikanayo ananena kuti: “Bwanji litakhala mawa? Ndilitu ndi mpata.” Tsiku lotsatira, lomwe linali Lachisanu, anayamba kuphunzira. Mlungu womwewo mtsikanayo anayamba kusonkhana ndipo anapitiriza kuphunzira.
5. Kodi tingasonyeze bwanji kuzindikira tikapempha munthu kuti tiziphunzira naye? (Onaninso zithunzi.)
5 N’zoona kuti si anthu onse omwe timawalalikira, amene amakhala okonzeka kuphunzira ngati mtsikana uja. Ena amafunika kuwathandizabe kuti chidwi chawo chiwonjezeke. Mwina pa ulendo woyamba tingafunike kukambirana nawo nkhani imene ingawasangalatse. Koma tikamapitiriza kukhala ndi maganizo abwino komanso kusonyeza munthu chidwi, sipangatenge nthawi kuti tiyambe kuphunzira naye. Ndiye kodi tinganene zotani popempha munthu kuti tiziphunzira naye? Abale ndi alongo ena omwe savutika kuyambitsa maphunziro a Baibulo anafunsidwa funso limeneli.
Kodi tingakambirane nkhani ziti ndi anthu a muzithunzizi, zomwe zingawathandize kuti ayambe kuphunzira Baibulo? (Onani ndime 5)a
6. Kodi tingapemphe bwanji munthu kuti tipitirize kukambirana naye?
6 Ofalitsa komanso apainiya amene anafunsidwa funsoli anafotokoza kuti m’mayiko ena zimakhala bwino kupewa mawu ena monga “kuphunzira,” “phunziro la Baibulo” kapena “kukuphunzitsani.” Iwo anati amangogwiritsa ntchito mawu ngati “kucheza, “kukambirana” kapena “kudziwa bwino Baibulo.” Kuti mupitirize kukambirana munganene kuti: “N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limayankha mafunso ofunika kwambiri pa moyo wathu” kapena, “Sikuti Baibulo langokhala buku lachipembedzo koma lingatithandize pa moyo wathu.” Mwina mungawonjezerenso kuti, “Sikuti zimafuna nthawi yambiri. Mungaphunzire mfundo zofunika pongokambirana kwa 10 kapena 15 minitsi.” Mungathe kulankhula zimenezi popanda kusonyeza kuti muzibwera mlungu uliwonse.
7. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe anthu ena anazindikira kuti apeza choonadi? (1 Akorinto 14:23-25)
7 Tiziwaitanira kumisonkhano. Zikuoneka kuti anthu ena mu nthawi ya Paulo anazindikira kwa nthawi yoyamba kuti apeza choonadi atapezeka pamisonkhano. (Werengani 1 Akorinto 14:23-25.) Anthu ambirinso masiku ano amapita patsogolo akayamba kusonkhana. Ndiye kodi ndi pa nthawi iti pamene tingawaitanire kumisonkhano? Mutu 10 wa buku la Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale umanena kuti tiziitanira kumisonkhano anthu amene timaphunzira nawo. Komabe, tisamadikire mpaka titafika mutuwu. Kungoyambira pamene tayamba kukambirana nawo, tingawaitanire kumisonkhano ya kumapeto kwa mlungu. Mwina tingawauze mutu wa nkhani ya onse kapena mfundo ina ya mu Phunziro la Nsanja ya Olonda ya mlungu umenewo.
8. Kodi ndi zinthu ziti zomwe tingafotokozere munthu tikamamuitanira kumisonkhano yathu? (Yesaya 54:13)
8 Tikamamuitanira munthu kumisonkhano, tizimufotokozera mmene misonkhanoyo imasiyanirana ndi zimene wakhala akuona kuzipembedzo zina. Wophunzira wina atafika pa Phunziro la Nsanja ya Olonda koyamba, anafunsa mphunzitsi wake kuti, “Ndiye kuti wochititsayo amadziwa dzina la aliyense?” Mlongoyo anayankha kuti, “Tonse timayesetsa kudziwana mayina ngati mmene timachitira ndi anthu a m’banja lathu.” Wophunzirayo anaona kuti izi ndi zosiyana ndi zimene zimachitika kutchalitchi kwawo. Anthu ambiri sadziwanso zimene zimachitika pamisonkhano yathu. (Werengani Yesaya 54:13.) Timasonkhana kuti tilambire Yehova, tiphunzitsidwe komanso tilimbikitsane. (Aheb. 2:12; 10:24, 25) Choncho misonkhano yathu imakhala yadongosolo komanso yothandiza, osati yongochitika mwamwambo. (1 Akor. 14:40) Ndipotu Nyumba za Ufumu zimamangidwa m’njira yakuti azikhala malo abwino ophunziriramo za Yehova. Sitimalowerera ndale ndipo sitimaona kuti chipani china ndi chabwino kuposa china. Sitichitanso zionetsero kapena kulowerera mikangano. Zingakhale bwino kuonetsa munthu amene timaphunzira naye Baibulo, vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? Iye angadziwiretu zimene adzaone akabwera ndipo zidzamuthandiza kusiyanitsa ndi zimene zimachitika kuchipembedzo chake.
9-10. Kodi tingathandize bwanji munthu kudziwa kuti sitikumukakamiza kulowa chipembedzo chathu kapena kupanga nawo zinthu zina? (Onani chithunzi.)
9 Anthu ena amaopa kubwera kumisonkhano yathu chifukwa amaganiza kuti tiwakakamiza kuti asiye chipembedzo chawo. Choncho tingauze munthu kuti timasangalala kulandira alendo ndipo sitiwakakamiza kuti azichita nawo zimene timachita pamisonkhano. Munthu angabwere ndi banja lake ngakhalenso ndi ana aang’ono. Ana salandira malangizo paokha, m’malomwake amakhala ndi makolo awo n’kumaphunzirira limodzi. Choncho makolo amadziwa kuti ana awo ndi otetezeka ndipo amadziwa zimene akuphunzira. (Deut. 31:12) Pamisonkhano sipayendetsedwa mbale ya zopereka kapena kupatsa anthu ma envelopu kuti aikemo ndalama. M’malomwake timatsatira lamulo la Yesu lakuti “Munalandira kwaulere, muzipereka kwaulere.” (Mat. 10:8) Tingamuuzenso munthuyo kuti safunika kuvala zodula kuti apezeke pamisonkhano chifukwa Mulungu amaona mumtima osati maonekedwe akunja.—1 Sam. 16:7.
10 Munthu akafika pamisonkhano muzimulandira bwino. Muzimuthandiza kuti adziwane ndi akulu komanso abale ndi alongo ena. Akaona kuti walandiridwa bwino akhoza kudzabweranso. Ngati iye alibe Baibulo, muzimuonetsa malemba m’Baibulo lanu kuti azitsatira zimene zikuphunziridwa.
Munthu amapindula kwambiri akayamba msanga kupezeka pamisonkhano (Onani ndime 9-10)
ZIMENE TINGACHITE TIKAYAMBA KUPHUNZIRA NDI MUNTHU
11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira munthu pa nkhani ya nthawi?
11 Tikayamba kuphunzira ndi munthu, tizikumbukira kuti munthuyo amakhalanso ndi zina zoti achite. Mwachitsanzo, muzisunga nthawi imene mwagwirizana ngakhale zitakhala kuti anthu a m’dera lanu sasunga nthawi. Mungachitenso bwino kuphunzira naye kwa nthawi yochepa pa ulendo woyamba. Ofalitsa ena aluso amanena kuti ndi bwino kuphunzira zochepa ngakhale munthuyo atanena kuti akufuna kuphunzira zambiri. Muzimulola kufotokoza maganizo ake ndipo musamalankhule kwambiri.—Miy. 10:19.
12. Kodi cholinga chathu chizikhala chiyani tikangoyamba kuphunzira Baibulo ndi munthu?
12 Kungochokera pamene tayamba kuphunzira ndi munthu, tizimuthandiza kuti adziwe komanso ayambe kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu. Kuti izi zitheke, nthawi zonse tiziphunzitsa zochokera m’Baibulo osati m’maganizo mwathu. (Mac. 10:25, 26) Mtumwi Paulo ankathandiza anthu kuganizira kwambiri za Yesu Khristu, yemwe Yehova anamutuma kuti adzathandize anthu kudziwa Yehovayo komanso kumukonda. (1 Akor. 2:1, 2) Paulo anasonyezanso kufunika kothandiza ophunzira atsopano kuti akhale ndi makhalidwe abwino omwe tingawayerekezere ndi golide, siliva ndiponso miyala yamtengo wapatali. (1 Akor. 3:11-15) Makhalidwewa akuphatikizapo chikhulupiriro, nzeru, kuzindikira komanso kuopa Yehova. (Sal. 19:9, 10; Miy. 3:13-15; 1 Pet. 1:7) Choncho tizitsanzira Paulo pothandiza anthu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Atate wawo wakumwamba.—2 Akor. 1:24.
13. Kodi tingasonyeze bwanji kuleza mtima komanso kumvetsa tikamaphunzira ndi munthu? (2 Akorinto 10:4, 5) (Onaninso chithunzi.)
13 Tikamaphunzitsa munthu tizitsanzira Yesu pokhala oleza mtima komanso omvetsa. Tizipewa kufunsa mafunso amene angamuchititse manyazi. Nthawi zina mungasiye mfundo zimene zikumuvuta kumvetsa kuti mudzakambirane pambuyo pake. M’malo momukakamiza kuti avomereze mfundo inayake imene sanaimvetse, tizimupatsa nthawi yokwanira kuti aiganizire n’kuivomereza. (Yoh. 16:12; Akol. 2:6, 7) Baibulo limayerekezera ziphunzitso zabodza ndi zinthu zozikika molimba. (Werengani 2 Akorinto 10:4, 5.) Kuti munthu asiye kukhulupirira zimene wakhala akuzikhulupirira, choyamba tiyenera kumuthandiza kuti azidalira kwambiri Yehova.—Sal. 91:9.
Muzimupatsa wophunzira nthawi yoganizira mfundo zina n’kuzivomereza (Onani ndime 13)
MMENE TINGALANDIRIRE ANTHU ATSOPANO AMENE ABWERA KUMISONKHANO
14. Kodi tiziwalandira bwanji anthu atsopano amene abwera kumisonkhano?
14 Yehova amafuna kuti tizilandira mopanda tsankho anthu atsopano amene abwera kumisonkhano popanda kuganizira chikhalidwe, mtundu kapenanso zimene ali nazo. (Yak. 2:1-4, 9) Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda alendo amene abwera kumisonkhano?
15-16. Kodi tingathandize bwanji atsopano kuti azimasuka pamisonkhano yathu?
15 Anthu ena amabwera kumisonkhano yathu kuti adzangoona mmene zimachitikira pomwe ena amakhala atauzidwa ndi munthu wa kudera lina. Choncho tikaona munthu wachilendo tizimulankhula. Tizimulandira bwino koma mosakokomeza zinthu. Tingamupemphe kuti akhale pafupi nafe. Tingamawerenge naye Baibulo kapena mabuku athu, apo ayi tingamupezere Baibulo kapena mabuku. Mungaganizirenso zinthu zina zimene zingamuthandize kukhala womasuka. Munthu wina atafika ku Nyumba ya Ufumu anauza m’bale amene anamulandira kuti ankaona kuti sanavale bwino ngati abale ndi alongo ena. M’baleyo anamuthandiza kukhala womasuka. Anamufotokozera kuti ngakhale kuti a Mboni amavala choncho, si osiyana ndi wina aliyense. Munthuyo anaphunzira mpaka kufika pobatizidwa ndipo sanaiwale mmene m’baleyu anamuthandizira. Koma tikamalankhula ndi alendo amene abwera kumisonkhano tizikhala osamala. Tisamawafunse mafunso amene angawachititse manyazi kapena okhala ngati tikuwafufuza.—1 Pet. 4:15.
16 Tingathandize anthu amene abwera kumisonkhano kukhala omasuka tikamalankhula mwaulemu zinthu zokhudza iwowo kapena zimene amakhulupirira. Tingachite izi pocheza, popereka ndemanga kapena pokamba nkhani. Tizipewa mawu amene angawakhumudwitse kapena amene angaoneke ngati tikuwanyoza. (Tito 2:8; 3:2) Mwachitsanzo, sitiyenera kunyoza mfundo zimene ena amakhulupirira. (2 Akor. 6:3) Abale amene amakamba nkhani za onse ayenera kukhala osamala pa nkhaniyi. Iwo angasonyeze kuti amaganizira anthu omwe si a Mboni, pofotokozera mawu amene anthuwo sangawamvetse bwino.
17. Kodi cholinga chathu chizikhala chotani tikapeza ‘anthu amene ali ndi maganizo abwino’ mu utumiki?
17 Tsiku lililonse likamadutsa, nthawi yoti tigwire ntchito yophunzitsa anthu imakhala ikuchepa. Choncho tipitirize kufufuza ‘anthu amene ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Tikawapeza, tisamachedwe kuyamba kuphunzira nawo kapena kuwaitanira kumisonkhano. Tikamatero, tidzawathandiza kuti ayambe kuyenda pa “msewu wopita ku moyo.”—Mat. 7:14.
NYIMBO NA. 64 Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala
a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Abale awiri akulankhula ndi msilikali amene anapuma pantchito yemwe wakhala pakhonde lake; alongo awiri akulalikira mwachidule kwa mayi amene watanganidwa.