Bolivia: Abale akumanga ofesi ya omasulira m’chinenero cha Chiayimara ku El Alto
Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi
BAIBULO limasonyeza kuti Mulungu adzachita zinthu zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito Ufumu wake. Ndipo lemba la Yesaya 9:7 limati, “Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.” Nayenso Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumuwu, anagwira ntchito modzipereka kwambiri pamene ankachita utumiki wake padziko lapansi. (Yoh. 2:17) Malipoti ali m’munsiwa akusonyeza kuti nawonso a Mboni za Yehova padziko lonse akutengera chitsanzo cha Yehova komanso Yesu. Iwo akuthandiza anthu kuona chikondi chimene Atate wathu Yehova, amatisonyeza.
El salvador: Msonkhano wachigawo wa 2015