Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 40
  • N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Mungakonde Kumvetsa Zimene Baibulo Limaphunzitsa?
    Galamukani!—2017
  • Kodi “Makiyi a Ufumu” N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?
    Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 40
Mzimayi akuwerenga Baibulo.

N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?

Yankho la m’Baibulo

M’Baibulo muli mfundo zotithandiza kuti tilimvetse. Kaya ndife anthu otani, uthenga wa Mulungu umene uli m’Baibulo ‘si wovuta kutsatira, ndipo si wapatali.’—Deuteronomo 30:11.

Mfundo zimene zingakuthandizeni kumvetsa Baibulo

  1. Muzikhala ndi maganizo oyenera. Muziona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Muzikhala ndi mtima wodzichepetsa popeza Mulungu amatsutsa odzikweza. (1 Atesalonika 2:13; Yakobo 4:6) Koma musamangokhulupirira zinthu popanda umboni chifukwa Mulungu amafuna kuti muzigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza.”—Aroma 12:1, 2.

  2. Muzipempha nzeru. Pa Miyambo 3:5, Baibulo limati: “Usadalire luso lako lomvetsa zinthu.” M’malomwake, ‘tizipempha kwa Mulungu’ kuti atipatse nzeru zotithandiza kumvetsa Baibulo.—Yakobo 1:5.

  3. Muziphunzira nthawi zonse. Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kwambiri ngati mumaliphunzira nthawi zonse osati modumphadumpha.—Yoswa 1:8.

  4. Muziphunzira mwadongosolo. Njira yabwino kwambiri yophunzirira Baibulo n’kufufuza zimene Malemba amanena pa nkhani inayake. Muziyamba ndi nkhani zosavuta kenako n’kufufuza nkhani zovutirapo. (Aheberi 6:1, 2) Mukamayerekezera lemba lina ndi linzake mudzaona kuti Baibulo limafotokoza lokha zinthu, ngakhale “zinthu zina zovuta kuzimvetsa.”—2 Petulo 3:16.

  5. Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipempha anthu ena kutithandiza kumvetsa Baibulo. (Machitidwe 8:30, 31) A Mboni za Yehova amaphunzitsa anthu Baibulo mwaulere. Mofanana ndi zimene Akhristu oyambirira ankachita, iwo amagwiritsa ntchito malemba pothandiza anthu kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni.—Machitidwe 17:2, 3.

Zinthu zimene si zofunika

  1. Nzeru kapena maphunziro apamwamba. Atumwi 12 a Yesu ankamvetsa Malemba ndiponso kuwaphunzitsa ngakhale kuti anthu ena ankawaona kuti ndi “osaphunzira ndiponso anthu wamba.”—Machitidwe 4:13.

  2. Ndalama. Mukhoza kuphunzira Baibulo popanda kulipira chilichonse. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena