Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwfq nkhani 41
  • Kodi Bungwe Lolamulira ndi Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Bungwe Lolamulira ndi Chiyani?
  • Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ndi ndani amene ali m’bungwe limeneli?
  • Kodi bungweli limayendetsa bwanji ntchito zake?
  • Kodi ndi ndani amene amathandiza pa ntchito za bungweli?
  • Tizilemekeza Kwambiri Abale Ngati Amenewa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Ntchito Zake
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
ijwfq nkhani 41
A m’Bungwe Lolamulira ali ndi othandiza awo pamsonkhano

Kodi Bungwe Lolamulira ndi Chiyani?

Bungwe Lolamulira ndi kagulu ka Akhristu olimba mwauzimu amene amayang’anira gulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova. Ntchito imene amagwira ili ndi mbali ziwiri:

  • Amayang’anira ntchito yokonza malangizo ochokera m’Baibulo amene amapezeka m’mabuku, pamisonkhano ndiponso m’masukulu a Mboni za Yehova.​—Luka 12:42.

  • Amayang’aniranso ntchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova. Amachita zimenezi potsogolera ntchito yolalikira ndiponso poonetsetsa kuti zopereka za anthu zikugwiritsidwa bwino ntchito.

Bungwe Lolamulira limatsatira chitsanzo cha “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu” amene ankasankha zinthu zofunika zokhudza mpingo wonse wa Chikhristu. (Machitidwe 15:2) Koma mofanana ndi atumwi ndi akulu okhulupirikawo, a m’bungweli si atsogoleri a gulu la Mboni za Yehova. Iwo amatsogoleredwa ndi mfundo za m’Baibulo ndipo amadziwa kuti Yehova Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti akhale Mutu wa mpingo wa Chikhristu.​—1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23.

Kodi ndi ndani amene ali m’bungwe limeneli?

Panopa m’bungweli muli a Kenneth Cook, Jr., Gage Fleegle, Samuel Herd, Geoffrey Jackson, Jody Jedele, Stephen Lett, Gerrit Lösch, Jacob Rumph, Mark Sanderson, David Splane, ndi Jeffrey Winder. Iwo amatumikira kulikulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse ku Warwick, New York ku United States.

Kodi bungweli limayendetsa bwanji ntchito zake?

Bungwe Lolamulira linakhazikitsa makomiti 6 omwe amayang’anira mbali zosiyanasiyana za ntchito ya Mboni za Yehova. Aliyense wa m’bungweli amakhala m’komiti imodzi kapena angapo.

  • Komiti ya Ogwirizanitsa: Imathandiza pa nkhani zokhudza malamulo, ngozi zamwadzidzidzi komanso kuzunzidwa kwa a Mboni chifukwa cha zimene amakhulupirira.

  • Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli: Imayang’anira zinthu zokhudza anthu amene amatumikira pa Beteli.

  • Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku: Imayang’anira ntchito yosindikiza ndi yotumiza mabuku athu komanso yomanga Nyumba za Ufumu, malo a misonkhano, maofesi a omasulira mabuku ndiponso nyumba za maofesi a nthambi.

  • Komiti ya Utumiki: Imayang’anira ntchito yathu yolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’​—Mateyu 24:14.

  • Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa: Imayang’anira ntchito yokonza malangizo ochokera m’Baibulo amene amapezeka pamisonkhano, m’masukulu, m’mavidiyo ndiponso m’zinthu zomvetsera zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

  • Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku: Imayang’anira ntchito yokonza malangizo ochokera m’Baibulo amene amapezeka m’mabuku, m’magazini ndiponso pawebusaiti yathu. Imayang’aniranso ntchito yomasulira mabuku.

Kuwonjezera pa ntchito zimene makomitiwa amagwira, Bungwe Lolamulira limakumana mlungu uliwonse kuti likambirane zofunika kuchita m’gulu la Mboni za Yehova. Pamisonkhanoyi anthu a m’bungweli amakambirana zimene Baibulo limanena ndipo amalola kuti mzimu woyera wa Mulungu uziwatsogolera kuti azisankha zochita mogwirizana.​—Machitidwe 15:25.

Kodi ndi ndani amene amathandiza pa ntchito za bungweli?

Akhristu okhulupirika a Mboni za Yehova ndi amene amathandiza pa ntchito za makomiti a Bungwe Lolamulira. (1 Akorinto 4:2) Akhristuwa ali ndi luso komanso amadziwa zambiri zokhudza ntchito imene imayang’aniridwa ndi komiti imene amathandiza. Iwo amachita nawo msonkhano wa komitiyo mlungu uliwonse. Ngakhale kuti sasankha nawo zochita, amaperekapo maganizo awo, amaonetsetsa kuti zimene komitiyo yasankha zizitsatiridwa komanso amaona mmene zomwe zasankhidwazo zikuyendera. Nthawi zina Bungwe Lolamulira limawatumizanso kumayiko osiyanasiyana kuti akaone mmene ntchito yapadziko lonse ikuyendera. Komanso angapatsidwe nkhani zoti akakambe pamsonkhano wapachaka kapena pamwambo wa omaliza Sukulu ya Giliyadi.

MAYINA A OTHANDIZA BUNGWE LOLAMULIRA

Komiti

Dzina

ya Ogwirizanitsa

  • Ekrann, John

  • Gillies, Paul

  • Snyder, Troy

Yoona za Atumiki a pa Beteli

  • Grizzle, Gerald

  • LaFranca, Patrick

  • Molchan, Daniel

  • Scott, Mark

  • Walls, Ralph

Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku

  • Butler, Robert

  • Corkern, Harold

  • Glockentin, Gajus

  • Gordon, Donald

  • Luccioni, Robert

  • Reinmueller, Alex

  • Sinclair, David

ya Utumiki

  • Breaux, Gary

  • Dellinger, Joel

  • Georges, Betty

  • Griffin, Anthony

  • Hyatt, Seth

  • Mavor, Christopher

  • Perla, Baltasar, Jr.

  • Smith, Jonathan

  • Turner, William, Jr.

  • Weaver, Leon, Jr

Yoona za Ntchito Yophunzitsa

  • Banks, Michael

  • Curzan, Ronald

  • Flodin, Kenneth

  • Malenfant, William

  • Noumair, Mark

  • Schafer, David

Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku

  • Ahladis, Nicholas

  • Christensen, Per

  • Ciranko, Robert

  • Godburn, Kenneth

  • Mantz, James

  • Marais, Izak

  • Martin, Clive

  • Myers, Leonard

  • Smalley, Gene

  • van Selm, Hermanus

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena