Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 10/15 tsamba 3
  • Tizilemekeza Kwambiri Abale Ngati Amenewa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizilemekeza Kwambiri Abale Ngati Amenewa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Bungwe Lolamulira ndi Chiyani?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Ntchito Zake
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chilengezo
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 10/15 tsamba 3
Msonkhano wa abale a m’Bungwe Lolamulira

Tizilemekeza Kwambiri Abale Ngati Amenewa

KUYAMBIRA mu 1992, abale a m’Bungwe Lolamulira amasankha abale okhulupirika omwe ndi akulu kuti aziwathandiza.a Abalewa ndi a “nkhosa zina” ndipo amachita zambiri pothandiza m’makomiti a Bungwe Lolamulira. (Yoh. 10:16) Iwo amapezeka pa misonkhano ya komiti imene amathandizayo. Abalewa amapereka mfundo ndiponso maganizo awo pa misonkhanoyi, koma a m’Bungwe Lolamulira ndi amene amasankha zochita. Abale amenewa amaonetsetsa kuti zimene komiti yasankha zizichitika ndipo amagwira bwino ntchito iliyonse imene apatsidwa. Amapitanso ku misonkhano yapadera ndiponso ya mayiko limodzi ndi abale a m’Bungwe Lolamulira. Nthawi zina amapemphedwa kuti akhale oimira likulu la Mboni za Yehova n’kumayendera maofesi a nthambi.

M’bale wina amene wagwira ntchito yothandiza Bungwe Lolamulira kuyambira mu 1992 ananena kuti: “Ntchito imene ndimagwira imathandiza kuti abale a m’Bungwe Lolamulira azigwira ntchito zina zofunika kwambiri.” M’bale winanso amene wagwira ntchitoyi kwa zaka 20 anati: “Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kuthandiza abalewa ndipo sindinkayembekezera kuti ndingachite zimenezi.”

Bungwe Lolamulira lapatsa abale okhulupirikawa udindo waukulu ndipo limayamikira zimene amachita. Tiyeni tonse tizilemekeza kwambiri abale ngati amenewa.—Afil. 2:29.

a Kuti mudziwe ntchito za makomiti 6 a Bungwe Lolamulira, werengani bokosi lakuti “Mmene Bungwe Lolamulila Limayendetsera Zinthu za Ufumu” m’mutu 12 wa buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulira.

Abale Amene Amathandiza M’makomiti a Bungwe Lolamulira

Komiti ya Ogwirizanitsa

  • John Ekrann

  • Robert Wallen

Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli

  • Gerald Grizzle

  • Patrick LaFranca

  • Daniel Molchan

  • Ralph Walls

Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku

  • Don Adams

  • Robert Butler

  • Harold Corkern

  • Donald Gordon

  • Robert Luccioni

  • Alex Reinmueller

  • David Sinclair

Komiti ya Utumiki

  • Gary Breaux

  • Joel Dellinger

  • Seth Hyatt

  • Christopher Mavor

  • Baltasar Perla, Jr.

  • William Turner, Jr.

  • Robert Wallen

  • Leon Weaver, Jr.

Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa

  • Ronald Curzan

  • Kenneth Flodin

  • William Malenfant

  • Mark Noumair

  • David Schafer

Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku

  • Robert Ciranko

  • James Mantz

  • Izak Marais

  • Gene Smalley

  • John Wischuk

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena