Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 112
  • Kodi Mawu Akuti Kumwamba Amatanthauza Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mawu Akuti Kumwamba Amatanthauza Chiyani?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Kumwamba N’kotani?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kumwamba
    Galamukani!—2016
  • Mzimu Woyera Ukugwira Ntchito m’Malo Osaoneka a Kumwamba
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Mafunso Okhudza Mmene Zilili Kumwamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 112
Dzuwa likuwala pamwamba pamitambo

Kodi Mawu Akuti Kumwamba Amatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

M’Baibulo, mawu akuti “kumwamba” amagwiritsidwa ntchito poimira zinthu zitatu: (1) kumwamba kumene timaona; (2) malo omwe kumakhala zolengedwa zauzimu; ndipo (3) chizindikiro cha malo okwezeka. Komabe, munthu angathe kudziwa tanthauzo loyenera la mawuwa malinga ndi nkhani imene akupezekamo.a

  1. Kumwamba kumene timaona. Apa, “kumwamba” kukutanthauza mbali ya dziko komwe mphepo imaomba, mbalame zimauluka, mitambo imapanga mvula ndi chipale chofewa ndiponso komwe kumaoneka ziphaliwali. (Salimo 78:26; Miyambo 30:19; Yesaya 55:10; Luka 17:24) Liwuli lingatanthauzenso kuthambo komwe kuli “dzuwa, mwezi ndi nyenyezi.”​—Deuteronomo 4:19; Genesis 1:1.

  2. Malo omwe kumakhala zolengedwa zauzimu. Mawu akuti “kumwamba” amatanthauzanso malo amene kumakhala zolengedwa zauzimu ndipo ndi kutali kwambiri kuposa kumwamba komwe timaona ndi maso. (1 Mafumu 8:27; Yohane 6:38) Kumeneku n’kumene kumakhala Yehova Mulungu, yemwe ndi “Mzimu,” komanso angelo omwe ndi zolengedwa zauzimu. (Yohane 4:24; Mateyu 24:36) Nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “kumwamba,” ponena za angelo, omwe ndi “mpingo wa oyera.”—Salimo 89:5-7.

    Baibulo limagwiritsanso ntchito mawu oti “kumwamba” ponena za mbali ya malo enieni amene Yehova amakhala, omwe ndi ‘malo ake okhala okhazikika.’ (1 Mafumu 8:43, 49; Aheberi 9:24; Chivumbulutso 13:6) Mwachitsanzo, Baibulo linaneneratu kuti Satana adzachotsedwa kumwamba limodzi ndi ziwanda zake ndipo sadzaloredwanso kupita kumalo enieni amene Yehova amakhala. Komabe, iwo akadali zolengedwa zauzimu.—Chivumbulutso 12:7-9, 12.

  3. Chizindikiro cha malo okwezeka. Malemba amagwiritsanso ntchito mawu akuti “kumwamba” kutanthauza malo okwezeka, ndipo nthawi zambiri mawuwa amanena za olamulira. Olamulira amenewa akhoza kukhala:

    • Yehova Mulungu yemwe ndi Mfumu yamphamvu ya chilengedwe chonse.—2 Mbiri 32:20; Luka 15:21.

    • Ufumu wa Mulungu womwe udzalowe m’malo mwa ulamuliro wa anthu. Baibulo limanena kuti Ufumu umenewu ndi “kumwamba kwatsopano.”—Yesaya 65:17; 66:22; 2 Petulo 3:13.b

    • Akhristu ena omwe ali padziko lapansi ndipo ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba.—Aefeso 2:6.

    • Maboma a anthu omwe olamulira ake amadzikweza kwambiri kuposa anthu amene akuwalamulira.—Yesaya 14:12-14; Danieli 4:20-22; 2 Petulo 3:7.

    • Mizimu yoipa imene panopa ikulamulira dzikoli.—Aefeso 6:12; 1 Yohane 5:19.

Kodi kumwamba n’kotani?

Kumwamba komwe kumakhala zolengedwa zauzimu kumachitika ntchito zosiyanasiyana. Zolengedwazi ndi angelo ambirimbiri “ochita zimene [Yehova] wanena.”—Salimo 103:20, 21; Danieli 7:10. Baibulo limasonyeza kuti kumwamba n’kowala kwambiri. (1 Timoteyo 6:15, 16) Mneneri Ezekieli anaona masomphenya osonyeza kumwamba kowala monyezimira, pomwe masomphenya akumwamba amene Danieli anaona anali ndi “mtsinje wa moto.” (Ezekieli 1:26-28; Danieli 7:9, 10) Kumwamba n’koyera komanso n’kokongola.—Salimo 96:6; Yesaya 63:15; Chivumbulutso 4:2, 3.

Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza kumwamba zimasonyeza kuti n’kochititsa mantha. (Ezekieli 43:​2, 3) Komabe, n’zosatheka kuti anthu adziwe bwinobwino mmene kumwamba kulili chifukwa chakuti kumakhala zolengedwa zauzimu zokhazokha.

a Mawu a Chiheberi amene amatanthauza “kumwamba” amachokera ku liwu limene limatanthauza “kutalika” kapena “pamwamba.” (Miyambo 25:3) Onani The New Brown, Driver, and Briggs Hebrew and English Lexicon of the Old Testament, tsamba 1029.

b Buku lina linanena kuti kumwamba kwatsopano kotchulidwa pa Yesaya 65:17 kumatanthauza “boma latsopano, ufumu watsopano.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia, voliyumu 4, tsamba 122.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena