Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 114
  • Kodi Pali “Machimo 7 Obweretsa Imfa?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali “Machimo 7 Obweretsa Imfa?”
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Tchimo N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”
    Yandikirani Yehova
  • Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tiziulula Ndiponso Kulapa Machimo Athu?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Tasiya Kuopa Tchimo?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 114
Munthu wosasangalala

Kodi Pali “Machimo 7 Obweretsa Imfa?”

Yankho la m’Baibulo

Baibulo silitchula mwachindunji mndandanda wa “machimo 7 obweretsa imfa.” Komabe, limaphunzitsa kuti anthu amene amachita machimo akuluakulu sadzapulumuka. Mwachitsanzo, Baibulo limati machimo akuluakulu monga dama, kupembedza mafano, kuchita zamizimu, kupsa mtima, komanso kumwa mwauchidakwa ndi “ntchito za thupi.” Komanso limati: “Anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—Agalatiya 5:19-21.a

Kodi Baibulo limatchula zinthu 7 zimene Mulungu amadana nazo?

Inde limatchula. Pa Miyambo 6:16, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu limati: “Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa.” Ngakhale zili choncho, mndandanda wa machimo womwe uli pa Miyambo 6:17-19, sukutanthauza kuti machimo onse ndi okhawa. M’malomwake, mavesiwa akungotchula magulu a zochita zomwe zikuimira zinthu zonse zolakwika, zimene zikuphatikizapo zoganiza, zolankhula, ndi zochita.b

Kodi mawu oti “tchimo lakupha” amatanthauza chiyani?

Mabaibulo ena amagwiritsa ntchito mawu amenewa pa lemba la 1 Yohane 5:16. Mwachitsanzo, Baibulo la The New American Bible limati: “Pali tchimo lobweretsa imfa.” Mawu akuti “tchimo lakupha” akhoza kumasuliridwanso kuti “tchimo lobweretsa imfa.” Kodi pali kusiyana kotani pakati pa “tchimo lobweretsa imfa” ndi “tchimo losabweretsa imfa”?—1 Yohane 5:16.

Baibulo limanena momveka bwino kuti machimo onse amabweretsa imfa. Komabe, nsembe ya dipo ya Yesu Khristu ikhoza kutipulumutsa ku uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12; 6:23) Choncho, “tchimo lobweretsa imfa” ndi limene silingakhululukidwe ndi nsembe ya dipo ya Khristu. Munthu amene amachita tchimo la mtundu umenewu amapitirizabe kulichita ndipo zimakhala zovuta kuti asinthe maganizo kapena makhalidwe ake. Baibulo limanena kuti munthu wochita tchimo limeneli “sadzakhululukidwa.”—Mateyu 12:31; Luka 12:10.

Kodi mndandanda wa machimo 7 obweretsa imfa unachokera kuti?

“Machimo 7 obweretsa imfa” poyambirirapo anali pa mndandanda wa zinthu 8 zomwe zinali zoipa kwambiri. Mndandandawu unapangidwa mu 300 C.E., ndi Evagrius Ponticus ndipo unathandiza kwambiri wansembe wina dzina lake John Cassian polemba mabuku ake. Mu 500 C.E., Papa Gregory Woyamba anasintha mndandanda wa zinthu 8 zomwe Cassian analemba n’kukhala mndandanda wa machimo 7 obweretsa imfa, kapena kuti machimo akuluakulu womwe tchalitchi cha Katolika chinayamba kuphunzitsa. Machimowa ndi: kunyada, umbombo, chilakolako cha mphamvu cha kugonana, nsanje, kususuka, mkwiyo ndiponso ulesi. Gregory ankaona kuti machimowa ndi akuluakulu kwambiri omwe amayambitsa machimo ena ambiri.

a Sikuti machimo otchulidwa pa Agalatiya 5:19-21 ndi okhawa omwe ndi akuluakulu, chifukwa pambuyo potchula machimo amenewa, Baibulo limanenanso kuti “ndi zina zotero.” Izi zikutanthauza kuti aliyense ayenera kugwiritsa ntchito luso la kuzindikira kuti apeze makhalidwe enanso oipa omwe sanatchulidwe.

b Lemba la Miyambo 6:16 lili ndi chitsanzo cha mawu a Chiheberi omwe amatsindika kwambiri za nambala yachiwiri poisiyanitsa ndi nambala yoyamba. Kutchula zinthu m’njira imeneyi kumapezeka kawirikawiri m’Malemba.—Yobu 5:19; Miyambo 30:15, 18, 21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena