Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwwd nkhani 8
  • Guluu wa Kanyama Kotchedwa Barnacle

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Guluu wa Kanyama Kotchedwa Barnacle
  • Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Moyo Wosatha pa Dziko Lapansi Umatipatsa
    Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Khungu la Nangumi Lotha Kudziyeretsa Lokha
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Guluu wa Nyongolotsi Yam’madzi
    Galamukani!—2011
  • Timadzi Tomata Kwambiri ta Nkhono
    Kodi Zinangochitika Zokha?
Onani Zambiri
Kodi Zinangochitika Zokha?
ijwwd nkhani 8
Ma Barnacle

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Guluu wa Kanyama Kotchedwa Barnacle

Asayansi akhala akuchita chidwi ndi kanyama kena kam’madzi kotchedwa Barnacle kamene kamamatirira kwambiri pamiyala, madoko ngakhalenso pasitima zam’madzi. Anthu amanena kuti guluu wa kanyamaka amamata mwamphamvu kwambiri kuposa guluu aliyense wopangidwa ndi anthu. Posachedwapa, asayansi atulukira zimene zimathandiza kuti guluuyu azimata kwambiri.

Taganizirani izi: Asayansi atulukira kuti kanyamaka kamayamba kafufuza malo abwino amene kangakhalepo. Kakawapeza, kamatulutsa timadzi tamitundu iwiri. Toyamba timakhala tamafuta ndipo timathandiza kuchotsa madzi pamalopo komanso kuti timadzi tachiwiri timate bwinobwino. Timadzi tachiwiriti timakhala tamapulotini.

Timadzi tamitundu iwiriti tikasakanikirana timapanga guluu wamphamvu kwambiri moti ngakhale mabakiteriya sangamuwononge. Guluu wamphamvuyu amathandiza kwambiri kanyamaka kuti kasachoke pamalowo kwa moyo wake wonse.

Tinyamati komanso chithunzi cha guluu wake chitakulitsidwa kwambiri

Tinyamati komanso chithunzi cha guluu wake chitakulitsidwa kwambiri

Luso lopanga guluu ameneyu ndi lovuta kwambiri kuposa mmene asayansi ankaganizira poyamba. Mmodzi mwa anthu amene anatulukira zimenezi anati: “Luso lopezeka m’chilengedweli, lothandiza kumata zinthu pamalo amene pali madzi, ndi lapadera kwambiri.” Zimene asayansi apezazi zikhoza kuwathandiza kupanga guluu amene angagwiritsidwe ntchito m’madzi, pazipangizo zamakono komanso m’thupi.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kanyamaka kazipanga guluu wamphamvu chonchi? Kapena kanyamaka kanachita kulengedwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena