25 Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe. Mulitali mwake linali masentimita 45, mulifupi mwake masentimita 45. Mbali zake zonse 4 zinali zofanana, ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 90. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.+