13 Ndipo pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense, yemwe ndi nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa,+ nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, muziperekanso nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.