6 Munthuyo azikhala mumzindawo mpaka atakaonekera pamaso pa oweruza,+ ndipo azikhalabe komweko mpaka mkulu wa ansembe amene alipo pa nthawiyo atafa.+ Zikatero, wopha munthuyo akhoza kubwerera nʼkukalowa mumzinda wa kwawo komwe anathawa kuja, nʼkumakhala mʼnyumba mwake.’”+