28 Ndiyeno Gaala mwana wa Ebedi anati: “Abimeleki ndi ndani, ndipo Sekemu ndi ndani kuti timʼtumikire? Kodi iye si mwana wa Yerubaala,+ ndipo mtumiki wake si Zebuli? Zitumikirani ana a Hamori, bambo a Sekemu. Koma ifeyo tizitumikira Abimeleki chifukwa chiyani?