-
2 Mbiri 22:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Koma Yehosabati mwana wamkazi wa mfumu, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pagulu la ana aamuna a mfumu amene ankayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi ndi mayi amene ankamusamalira nʼkukamubisa mʼchipinda chamkati chogona. Yehosabati, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu,+ (ameneyu anali mkazi wa wansembe Yehoyada+ komanso mchemwali wake wa Ahaziya) anakwanitsa kubisa mwanayo kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe.+
-