14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa.
Iwo akuchita chigololo+ ndiponso akuchita zinthu mwachinyengo.+
Akulimbikitsa anthu ochita zoipa
Ndipo sakusiya zinthu zoipa zimene akuchita.
Kwa ine, onsewo ali ngati Sodomu+
Ndipo anthu okhala mumzindawu ali ngati Gomora.”+