-
Yeremiya 50:44Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
44 Taona! Wina adzabwera ngati mkango kuchokera munkhalango zowirira zamʼmphepete mwa Yorodano. Adzabwera kudzaukira malo otetezeka odyetserako ziweto, koma mʼkanthawi kochepa ndidzawathamangitsa* pamalowo. Ndidzaika pamalopo mtsogoleri amene ndamusankha.+ Chifukwa ndi ndani amene angafanane ndi ine ndipo ndi ndani angatsutsane nane? Kodi pali mʼbusa amene angakane kuchita zimene ine ndikufuna?+
-