7 Chipinda cha alonda chilichonse chinali bango limodzi mulitali ndi bango limodzi mulifupi. Kuchoka pachipinda chimodzi kukafika pachipinda china panali mikono 5.+ Malo apafupi ndi khomo la kanyumbako, pafupi ndi khonde limene linayangʼanizana ndi kachisi, anali bango limodzi.