16 Mukutsatira malamulo a Omuri komanso zinthu zonse zimene anthu a mʼnyumba ya Ahabu amachita.+
Ndipo mukuyendera malangizo awo.
Nʼchifukwa chake ndidzakusandutsani chinthu chodabwitsa,
Ndipo anthu amumzindawo adzakhala oyenera kuwaimbira mluzu.+
Inuyo mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”+