27 Nʼzoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Chifukwa ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti nawonso ayenera kutumikira oyerawo powapatsa zinthu zofunika pa moyo.+