18 Mngelo winanso anatuluka kuguwa lansembe ndipo anali ndi ulamuliro pa moto. Iye analankhula mofuula ndi mngelo amene anali ndi chikwakwa chakuthwa uja kuti: “Tsitsa chikwakwa chako chakuthwacho nʼkumweta mpesa wapadziko lapansi ndipo usonkhanitse pamodzi maphava ake chifukwa mphesazo zapsa.”+