14 Ndipo pa nthawi ya chakudya Boazi anaitana Rute kuti: “Tabwera kuno udzadye mkate+ ndiponso uziusunsa mu vinyo wowawasayu.” Choncho Rute anadzakhala pansi limodzi ndi okololawo, ndipo Boazi anali kum’patsira mbewu zokazinga,+ iye n’kumadya moti anakhuta mpaka zina kutsala.