Salimo 112:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+ צ [Tsa·dhehʹ]Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ק [Qohph]Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+ Miyambo 22:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+ Yesaya 58:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+ ndiponso kuti muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala.+ Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka+ ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.+ Ezekieli 18:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 ngati sazunza munthu aliyense,+ ngati amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ ngati salanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati amapatsa munthu wanjala chakudya+ ndi kuphimba munthu wamaliseche ndi chovala,+
9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+ צ [Tsa·dhehʹ]Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ק [Qohph]Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+
7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+ ndiponso kuti muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala.+ Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka+ ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.+
7 ngati sazunza munthu aliyense,+ ngati amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ ngati salanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati amapatsa munthu wanjala chakudya+ ndi kuphimba munthu wamaliseche ndi chovala,+