17 Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse pamodzi ndi kuwoloka Yorodano kupita kukakumana nawo n’kukafola kuti amenyane nawo.+ Atafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi Asiriya, Asiriyawo anayamba kumenyana naye.