15 Oimba,+ ana a Asafu,+ anali pa ntchito yawo mogwirizana ndi lamulo la Davide,+ la Asafu,+ la Hemani+ ndi la Yedutuni+ wamasomphenya+ wa mfumu. Alonda a pazipata+ anali pazipata zosiyanasiyana.+ Panalibe chifukwa choti asiyire ntchito yawo chifukwa abale awo Alevi anawakonzera+ nyama yawo.