2 Pali munthu amene Mulungu woona amam’patsa chuma, katundu, ndi ulemerero,+ ndiponso amene sasowa chilichonse chimene moyo wake umalakalaka,+ koma Mulungu woona samulola kudya zinthu zakezo,+ ndipo mlendo+ ndi amene amazidya. Zimenezi n’zachabechabe ndipo ndi nthenda yoipa.