Mlaliki
6 Pali zinthu zomvetsa chisoni zimene ndaona padziko lapansi pano, ndipo n’zofala pakati pa anthu: 2 Pali munthu amene Mulungu woona amam’patsa chuma, katundu, ndi ulemerero,+ ndiponso amene sasowa chilichonse chimene moyo wake umalakalaka,+ koma Mulungu woona samulola kudya zinthu zakezo,+ ndipo mlendo+ ndi amene amazidya. Zimenezi n’zachabechabe ndipo ndi nthenda yoipa. 3 Ngati munthu atabereka ana 100+ n’kukhala ndi moyo zaka zambirimbiri, masiku a moyo wake n’kukhala ochuluka,+ koma moyo wake osakhutira ndi zinthu zabwino,+ komanso osalowa m’manda,+ ndithu mwana amene anabadwa wakufa ali bwino kuposa iyeyu.+ 4 Pakuti mwanayu anangobadwira pachabe. Iye anapita mu mdima ndipo dzina lake lidzaphimbidwa ndi mdima.+ 5 Ngakhale dzuwa sanalione, kapena kulidziwa.+ Ameneyu ali ndi mpumulo kusiyana ndi woyamba uja.+ 6 Ngakhale munthu atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma sanasangalale ndi zabwino,+ kodi phindu lake n’chiyani? Pajatu aliyense amapita kumalo amodzi.+
7 Ntchito yonse imene anthu amaigwira mwakhama amagwirira pakamwa pawo,+ koma moyo wawo sukhuta. 8 Kodi munthu wanzeru amaposa bwanji munthu wopusa?+ Kodi munthu wovutika amapindula chiyani chifukwa chodziwa mmene angachitire zinthu ndi anthu? 9 Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.+ Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.+
10 Chilichonse chimene chinakhalapo chinapatsidwa kale dzina, ndipo zinadziwika kale kuti munthu ndi ndani.+ Iye sangathe kudziteteza pa mlandu wotsutsana ndi amene ali wamphamvu kuposa iyeyo.+
11 Chifukwa chakuti pali zambiri zoyambitsa zinthu zachabe,+ kodi munthu amapindula chiyani? 12 Ndani angadziwe zabwino zimene munthu angachite pa moyo wake,+ masiku onse a moyo wake wachabechabe, umene umakhala ngati mthunzi?+ Pakuti ndani angamuuze munthu zimene zidzachitike padziko lapansi pano iyeyo atafa?+