9 kuti aliyense wa iwo amasule wantchito wake wamwamuna kapena wamkazi, mwamuna wachiheberi+ kapena mkazi wachiheberi ndi kumulola kupita kwawo mwaufulu. Anachita izi kuti anthuwo asagwiritsenso ntchito Myuda mnzawo, amene ndi m’bale wawo ngati wantchito wawo.+