13 Iye anapitiriza kuyeza kanyumba ka pachipatako kuchokera padenga la chipinda chimodzi cha alonda kukafika padenga la chipinda china cha alonda ndipo anapeza mikono 25.+ Khomo la chipinda cha alonda cha mbali iyi linali moyang’anizana ndi khomo la chipinda cha mbali inayo.