24 Kenako ananditengera kumbali ya kum’mwera. Kumeneko ndinaonakonso kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kum’mwera.+ Iye anayeza zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake ndipo miyezo yake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba ta zipata zina zija.