8 Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu. Iwo adzakhala ngati mkango pakati pa nyama zakutchire. Adzakhala ngati mkango wamphamvu pakati pa magulu ankhosa, umene umati ukadutsa pakati pa nkhosazo, ndithu umazimbwandira ndi kuzikhadzula+ ndipo sipakhala wozipulumutsa.