3 Amuna amphamvu ovala zovala zofiira kwambiri afika. Anyamula zishango zonyika mu ututo wofiira.+ Pokonzekera nkhondo, iwo akukweza mikondo yawo yokhala ndi zogwirira zamtengo.+ Zida zawo zankhondo zachitsulo zimene zili pamagaleta awo zili waliwali ngati moto.