7 Chifukwa cha kuchuluka kwa mauthenga amene anaululidwa kwa ine, aliyense asandiganizire koposa mmene ayenera kundiganizira.
Chotero, kuti ndisadzikweze mopitirira muyezo,+ ndinapatsidwa munga m’thupi,+ mngelo wa Satana woti azindimenya nthawi zonse, kuti ndisadzikweze mopitirira muyezo.